Imaam Abu Hanifah Ndi Mafunso Atatu A Mfumu Ya Chiroma

Mfumu yachiroma ulendo wina inatumiza chuma chambiri kwa Khalifa (Mtsogoleri) wa asilamu. isanatumize nthumwi yake ndi chumacho, Mfumuyi inamulamula kuti akafunseko mafunso atatu kwa ma Ulama achisilamu.

Nthumwi yachiromayi monga idauzidwira, idafunsa mafunso atatu aja kwa ma Ulama koma sanathe kumupatsa mayankho okhutira.

Pa nthawiyo Imaam Abu Hanifah anali mnyamata wachichepele ndipo kudapezeka kuti anafika pamalopo ndi bambo ake.

Atawona kuti ma Ulama akulephera kuyankha mokwanira mafunso atatuwo, adapita kwa Khalifah ndikupempha chilolezo kuti ayankhe mafunso kwa nthumwi yachiromayi.

Khalifah adamulora ndipo adatembenukira kwa nthumwi yachiromayi yomwe idakhala pa guwa lapamwamba ndikuifunsa kuti: “Kodi inu ndi amene muzifunsa mafunso?”

Nthumwiyo itayankha motsimikiza, Imaam Abu Hanifah adati: “ngati ziri choncho inuyo mutsike kuti ine ndikhale paguwapo.

Nthumwiyo idavomera ndikutsika, ndikumulora Imaam Abu Hanifah kuti akhalepo.

Nthumwi yachiromayi kenako idapereka funso lake loyamba, “Kodi kudali ndani asanabwere Allah?” Imaam Abu Hanifah adayankha pogwiritsanso ntchito funso loti, “Kodi masamu mumawadziwa?” Munthuyo anayankha, “Eya.”

Imaam Abu Hanifah anapitiriza kunena kuti: “Kodi nambala yanji yomwe imabwera kumbuyo kwa 1?”

Munthuyo adayankha nati: “Nambala yoyamba ndi imodzi; palibe kalikonse pambuyo pake. Kenako Imaam Abu Hanifah adamaliza kuyankha kwake pofotokoza kuti: “Ngati palibe kalikonse pambuyo pa nambala wani, nchiyani chingakhalepo chilichonse pambuyo pa Allah?

Nthumwiyo inafunsanso funso lachiwiri. Adafunsa kuti: “Kodi Mulungu walunjika mbali iti?”

Apanso Imaam Abu Hanifah adayankha pofunsanso funso loti: “Mukayatsa nyali, kuwalako kumaunikira mbali iti?” nthumwiyo inayankha, “Kuwala kumawala mofanana kumbali zonse zinayi.”

Imaam Abu Hanifah adalongosola kuti: “Ngati kuunika komwe kungathe kuyatsidwa ndikuzimitsidwa ilibe mbali yeniyeni younika, kodi kuunika kwa Mlengi wa kumwamba ndi dziko lapansi, komwe kuli kosatha ndi kopambanitsitsa, kungakhale bwanji ndi malire enieni? ”

Kenako munthuyo adafunsa funso lake lachitatu komanso lomaliza: “Kodi Allah akuchita chiyani?”

Imaam Abu Hanifah adayankha: “Watsitsa paguwa munthu wosakhulupirira yemwe ndi inuyo, ndipo wamukweza munthu wokhulupirira yemwe ndi ineyo.”

Imaam Abu Hanifah adayankha bwino komanso moyenera mafunso onse atatu ndipo nthumwi yachiroma idavomereza kugonja ndikunyamuka.

Kukambitsirana kwa Imaam Abu Hanifah (rahimahullah) ndi gulu la Okana Mulungu

Gulu lina la anthu osakhulupirira mwa Allah linafika kwa Imaam Abu Hanifah (rahimahullah) ndi cholinga choipa chofuna kumupha.

Atawaona, Imaam Abu Hanifah (rahimahullah) adaganiza zokambirana nawo ndipo adawafunsa kuti:

“Ngati munthu atanati anene kuti waona ngalawa imene ilibe woyendetsa kapena woiwongolera ndi, ikudutsa m’mafunde a m’nyanja mowongoka kotheratu, ikunyamula katundu pagombe lina ndi kukamutsitsa pagombe lina; zonse pa zokha popanda munthu woti aziyang’anira ndi kuzilamulira, mungati chiyani?”

Nthawi yomweyo gululo linati, “Zochitika zoterezi n’zosamveka moti palibe munthu wanzeru amene angavomereze kuti zingatheke!”

Imaam Abu Hanifah (rahimahullah) adayankha nati: “Nanga nchiyani chachitika ndi luntha lanu? Pamene mukuvomereza kuti chombo chimodzi sichingayende popanda oyendetsa, ndiye mukuvomereza bwanji kuti chilengedwe chonse chingathe kugwira ntchito popanda Allah Ta’ala kuwongolera izo?”

Gulu lonse lidazizwa ndi malingaliro awa ndipo lidalapa nthawi yomweyo ndikuvomera Chisilamu pa maso pa Imaam Abu Hanifah (rahimahullah).

Check Also

Mariziq Ali M’manja Mwa Allah Yekha

Cholengedwa chilichonse chimafunikira kudya kuti chipitilire kukhala ndi moyo, ndipo chakudya chili m’manja mwa Allah …