Qadah ndi Salaam

7. Ngati ili qa’dah yomaliza, werengani tashahhud, Salawaat Ebrahimiyyah (Durood Ebrahim) ndipo kenako pangani duwa.

Duruud Ebrahimiyyah (Durood Ebrahim) ili motere:

اَللّٰهُمَّ صَلِّ عَلٰى مُحَمَّدٍ وَّعَلٰى اٰلِ مُحَمَّدٍ كَمَا صَلَّيْتَ عَلٰى إِبْرَاهِيْمَ وَعَلٰى اٰلِ إِبْرَاهِيْمَ وَبَارِكْ عَلٰى مُحَمَّدٍ وَّعَلٰى اٰلِ مُحَمَّدٍ كَمَا بَارَكْتَ عَلٰى إِبْرَاهِيْمَ وَعَلٰى اٰلِ إِبْرَاهِيْمَ فِيْ الْعَالَمِيْنَ إِنَّكَ حَمِيْدٌ مَّجِيْدٌ

Allaahummah swalli ‘alaa Muhammadi wa’alaa aali Muhammad kaa swallaita ‘alaa Ibrahiima wa’alaa aali Ibrahiim, wabaarik ‘alaa Muhammad wa’alaa aali Muhammad kamaa swallaita ‘alaa Ibrahiim wa’alaa aali Ibrahiim, fil ‘aalamiin innaka hamiidun majiid

O Allah! onetsani chifundo Chanu chapadera pa Sayyiduna Muhammad ndi kubanja la Sayyiduna Muhammad monga mudawachitira chifundo Chanu chapadera Sayyiduna Ebrahim ndi kubanja la Sayyiduna Ebrahim ndipo perekani madalitso anu apadera pa Sayyiduna Muhammad ndi kubanja la Sayyiduna Muhammad monga mwawapatsira madalitso anu apadera Sayyiduna Ebrahim ndi banja la Sayyiduna Ebrahim m’zolengedwa zonse (I. e mwa anthu anthawi zonse). Ndithu, Inu ndiinu Wotamandidwa ndiponso Wapamwambamwamba.

Mutha kuwerenganso dua iyi yomwe yatchuridwanso mu Hadith:

اَللّٰهُمَّ إِنِّيْ ظَلَمْتُ نَفْسِيْ ظُلْمًا كَثِيرًا وَلَا يَغْفِرُ الذُّنُوْبَ إِلاَّ أَنْتَ فَاغْفِرْ لِيْ مَغْفِرَةً مِّنْ عِنْدِكَ وَارْحَمْنِيْ إِنَّكَ أَنْتَ الْغَفُوْرُ الرَّحِيْم

Allaahumma inii dhwalamtu nafsii dhulman kathiirah walaa yaghfirudh dhunuuba illaa Anta faghfirlii maghfiratan min ‘indik warhamnii innaka Antal Ghafuur rahiim.

O Allah! Ndadzipsinja mopyola malire (pochita machimo), ndipo palibe amene angakhululuke machimo kusiya Inu, choncho ndikhululukireni ndi chikhululuko chapadera chochokera kumbali Yanu ndipo ndichitireni chifundo, ndithu, Inu nokha ndinu wokhululuka, Ngwachisoni.

8. Mukamaliza dua yanu, pangani salaam ponena kuti,

اَلسَّلَامُ عَلَيْكُمْ وَرَحْمَةُ اللهْ

Assalaam alaikum warahmatullaah.
kwinaku mukutembenuzira mutu wanu kumanja, ndi kenanso mukutembenuzira mutu wanu kumanzere.

9. Osatsitsa kapena kugwedeza mutu pamene ukupanga salaamu.

10. Tembenuzirani nkhope yanu mbali zonse kuti tsaya liwonekere kumbuyo.

11. Mukamaliza salamu, werengani أَسْتَغْفِرُ الله katatu.

12. Pangani ma dua (popeza ino ndi nthawi yolandiridwa ma dua).

13. Werengani Tasbeeh Faatimi pambuyo pa Swalaah iliyonse. Tasbiih faatwimii ndiko kuwerenga mawu oti Subhaanalla ka 33, Alhamdulillah ka 33 komanso Allaah akbar ka 33 ndikukwaniritsa kachi 100 powerenga mawu awa:

لَا إِلٰهَ إلَّا اللهُ وَحْدَهُ لَا شَرِيْكَ لَهُ لَهُ الْمُلْكُ وَلَهُ الْحَمْدُ وَهُوَ عَلٰى كُلِّ شَيْءٍ قَدِيْر

Laa ilaah illallaahu wahdahu laa shariika lah lahul mulku walahul hamdu wahuwa ‘alaa kuli shai-in qadiir

Palibe wopembedzedwa mwachoonadi koma Mulungu Yekha, yemwe alibe mnzake. Ulamuliro Ngwake (pa zachilengedwe zonse), ndipo kutamandidwa konse nkwa lye, ndipo lye Yekha ali ndi mphamvu Pachilichonse.

Check Also

Ruku ndi I’tidaal

6. Timisomali tamapazi onse awiri akhale pamodzi. Ngati izi ndizovuta, ndiye kuti ziyenera kusungidwa moyandikana …