Kukonzekera nkhondo ya Tabuuk

Abdur Rahmaan bun Khabbaab (radhwiyallah anhu) akufotokoza motere:

Ndinalipo pamene Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) ankawalimbikitsa ma Swahaabah (radhwiyallahu ‘anhum) kuti akonzekeretse asilikali ndi kutenga nawo gawo pa ulendo wa Tabuuk. Nthawi imeneyo Uthmaan (radhwiya allahu ‘anhu) adayimilira nati: “Oh Mthenga wa Allah (swallallaahu ‘alayhi wasallam)! Ine ndikupereka ngamila zana limodzi ndi zokhalira zake zonse Mnjira ya Allah.”

Pambuyo pake, Rasulullah (swallallaahu ‘alayhi wasallam) adawalimbikitsa maswahaabah (radhwiyalahu ‘anhum) kachiwiri kuti akonzekeretse asilikali kuti apite ku nkhondo ya Tabuuk. Uthman (radhwiyallahu anhu) adayimiliranso nati: “Oh Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam)!ndikupereka ngamila mazana awiri ndi zoyala pokhala pa ngamila ndi zopondera zake) m’njira ya Allah.” Kenako Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) adawalimbikitsa maswahaabah (radhwiyallahu ‘anhum) kuti apereke nawonso kachitatu. O, Mtumiki wa Allah (swallallaahu ‘alayhi wasallam)! Ndipereka ngamira zina mazana atatu ndi zoyala pokhala komanso zopondera mnjira ya Allah.(zomwe zidapangitsa chiwerengero cha ngamila zonse zomwe adapereka kufika pa mazana asanu ndi limodzi)”

Nthawi imeneyo, ndinamuona Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) akutsika pa mimbar uku ali osangalala kwambiri akunena kuti: “Uthmaan sadzachita chinthu china chabwino chilichonse pambuyo pa ntchito imeneyi (kugula Jannah yake), Uthmaan sadzayenera kuchita chinthu china chabwino pambuyo pa ntchito imeneyi.

Check Also

Muvi Oyamba kulasa Mchisilamu

Olemekezeka Sa’d (radhwiyallahu ‘anhu) adali m’gulu la ma Swahaabah omwe Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) adawatumiza …