Kugula Malo Oonjezera Musjid-ul-Haraam

Nthawi ina Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) adapita kwa munthu wina ku Makkah Mukarramah ndipo anati kwa iye, “O wakuti-ndi-wakuti! Kodi ungandigulitseko nyumba yako, kuti ndiwonjezereko nzikiti mozungulira Ka’bah, ndipo mu mphotho ya ntchito yabwinoyi, ndikukutsimikizira kuti udzakhala ndi nyumba yachifumu ku Jannah (kuwonjezera pa ndalama za nyumba yomwe utapatsidwe)?”

Munthuyo anayankha, “E, inu Mtumiki wa Allah (swallallaahu ‘alayhi wasallam)! Wallah, iyi ndi nyumba yokhayo yomwe ndili nayo!
Ndikakugulitsa, sindidzakhalanso nyumba yokhalamo ina ku Makkah Mukarramah.”

Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) adamulimbikitsanso munthuyo kuti: “Ngakhale uli nayo Ndigulitse nyumba yako kuti ndionjezere malo a mzikiti pozungulira Kaaba, ndi chifukwa cha ntchito yabwino imeneyi, ndikusungira nyumba yachifumu ku Jannah.” Munthuyo anayankha: “Ndikulumbira kwa Allah! Ine sindikufuna kugulitsa nyumba yanga.

Pambuyo pake Uthmaan (radhwiyallahu ‘anhu) adamva zomwe zidachitikazi choncho anapita kwa munthuyo yemwe adali bwenzi lake chisilamu chisanafike, ndipo adati: “Oh! Ndamvetsedwa kuti Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) amafuna kugula nyumba yako kuti ikulitse dera la mzikiti pozungulira Ka’aba, ndipo pobwezera zabwinozo, anakulonjeza kukhala ndi nyumba yachifumu ku Jannah. Mwakana izi?.” Munthuyo anayankha kuti, “Eya, ndinakana.”

Uthmaan (radhwiyallaahu ‘anhu) adapitiriza kumulimbikitsa kuti agulitse nyumba yake mpaka Patsogolo pake adavomera ndipo Uthmaan (radhwiyallahu ‘anhu) adamugula iye pa ndalama yokwana 10 000 dinar (ndalama zagolide).

Kenako Uthmaan (radhwiyallaahu ‘anhu) adapita kwa Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) Nati kwa iye: “E, Mtumiki wa Allah (swallallaahu ‘alayhi wasallam)! Ndinadziwa kuti mukufuna kugula nyumba ya wakuti-ndi-akuti, ndi chholinga chhofuuna kukulitsa malo a mzikiti mozungulira Ka’aba ndipo munamutsimikizira mwini nyumbayi kuti akapeza nyumba yachifumu ku Jannah. Nyumbayo tsopano ndi yanga, chifukwa ndagula kwa mwini wakeyo, kodi Mukuilandira kwa ine mwaulere ndikundipatsa nyumba yachifumu ku Jannah?”

Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wasallam) adayankha motsimikiza ndipo adalandira nyumbayo kuchokera kwa Uthmaan (Radhwiyallahu ‘anhu), kumutsimikizira nyumba yachifumu ku Jannah ndi kuwapanga ma Swahaabah
(Radhiyallahu ‘anhum) kukhala mboni pa zimenezo.

Check Also

Muvi Oyamba kulasa Mchisilamu

Olemekezeka Sa’d (radhwiyallahu ‘anhu) adali m’gulu la ma Swahaabah omwe Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) adawatumiza …