Dua ya Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) kwa Ali (radhwiyallahu ‘anhu) potumiza ku Yemen

Ali (radhwiyallahu ‘anhu) akuti:

Rasulullah (swallallaahu ‘alayhi wasallam) adanditumiza monga bwanamkubwa wake ku Yemen. Ndisananyamuke ndidalankhula naye ndipo ndidati: “E, Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam)! Inu mukunditumiza kwa anthu akuluakulu kuposa ine. Kuonjezera apo, ine ndiine mwana, ndipo ndilibe kuzindikira kulikonse pa kaweruzidwe kamilandu.

Atamva nkhawa zanga, Rasulullah (swallallaahu ‘alayhi wasallam) adayika dzanja lake lodalitsika pachifuwa panga ndipo adapanga dua motere:

اللهم ثبت لسانه واهد قلبه

O Allah! Likhazikitseni lirime lake (ponena Choonadi) ndipo mumuongole mtima wake (Kumbali ya chilungamo).

Pambuyo pake Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) adandiyankhula nati: “E, inu nonse! Magulu awiri akayambana, onetsetsani kuti mwamva mbali zonse ziwiri musadapereke chigamulo pa mlanduwo. Mukaugwira uphungu wangawu, mudzamvetsetsa bwino lomwe, ndipo mudzadziwa kupanga chiganizo ndi kuweruza moyenera pakati pawo.

Zanenedwa kuti chifukwa cha Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) kumupangira Dua Ali (radhiyallaahu ‘anhu) ndi kumulangiza zimenezi, Ali (radhwiyallahu ‘anhu) sadakumane ndi vuto lililonse poweruza pakati pa anthu.” (Musnad Ahmed #882)

Check Also

Muvi Oyamba kulasa Mchisilamu

Olemekezeka Sa’d (radhwiyallahu ‘anhu) adali m’gulu la ma Swahaabah omwe Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) adawatumiza …