Qunuut

3. Ndi sunnah kuswali Swalah ya Witr tsiku lililonse m’chaka chonse. Swalah ya Witri idzachitika mukatsiriza kuswali Fardh ndi Sunnah za Swalah ya Esha. M’chaka chonse, munthu akaswali Witr sangawerenge Qurnuot. Komabe zili sunnah kuwerenga Ounoot mu pa swala ya Witr mu theka lachiwiri la mwezi wa Ramadhaan (kuyambira pa 15 Ramadhaan mpaka kumapeto kwa Ramadhaan). Qunuut ya swalah ya Witr ndi:

اَللّٰهُمَّ إِنَّا نَسْتَعِيْنُكَ وَنَسْتَغْفِرُكَ وَنَسْتَهْدِيْكَ وَنُؤْمِنُ بِكَ وَنَتَوَكَّلُ عَلَيْكَ وَنُثْنِيْ عَلَيْكَ الْخَيْرَ كُلَّهُ نَشْكُرُكَ وَلَا نَكْفُرُكَ وَنَخْلَعُ وَنَتْرُكُ مَنْ يَّفْجُرُكَ اَللّٰهُمَّ إِيَّاكَ نَعْبُدُ وَلَكَ نُصَلِّيْ وَنَسْجُدُ وَإِلَيْك نَسْعٰى وَنَحْفِدُ نَرْجُوْ رَحْمَتَكَ وَنَخْشٰى عَذَابَكَ إِنَّ عَذَابَكَ الْجِدَّ بِالْكُفَّارِ مُلْحِقٌ

اَللّٰهُمَّ اهْدِنِيْ فِيْمَنْ هَدَيْتَ وَعَافِنِيْ فِيْمَنْ عَافَيْتَ وَتَوَلَّنِيْ فِيْمَنْ تَوَلَّيْتَ وَبَارِكْ لِيْ فِيْمَا أَعْطَيْتَ وَقِنِيْ شَرَّ مَا قَضَيْتَ إِنَّكَ تَقْضِيْ وَلَا يُقْضٰى عَلَيْكَ إِنَّهُ لَا يَذِّلُّ مَنْ وَّالَيْتَ وَلَا يَعِزُّ مَنْ عَادَيْتَ تَبَارَكْتَ رَبَّنَا وَتَعَالَيْتَ فَلَكَ الْحَمْدُ عَلٰى مَا قَضَيْتَ أَسْتَغْفِرُكَ وَأَتُوْبُ إِلَيْكَ وَصَلّٰى اللهُ عَلٰى النَّبِيِّ وآلِهِ

E, Allah Nditsogolereni pamodzi ndi amene mudawaongola, Ndipatseni chifewetse pamodzi ndi amene mudawafewetsa, Ndithandizeni pa zinthu zanga (ndipo ndithandizeni) pamodzi ndi amene mudawasamalira (ndikuwathandizira). Ndipatseni mabaraka (madalitso) m’zimene mwandipatsa, Ndipulumutseni ku zoipa zazomwe mudandilamula. Ndithu, Inu nokha ndi Yemwe Muweruzira (zochita za onse) ndipo palibe woweruza pa Inu. Amene ali pansi pa chitetezo Chanu, sanganyozedwe, ndipo amene Mwawachita kukhala mdani Wanu, sadzapatsidwa ulemu. Rabb wathu. Ndinu wodzaza ndi madalitso ndi Wammwambamwamba. Kuyamikidwa konse nkwa Inu nokha chifukwa cha ziganizo zomwe mwapanga. Ndikukupemphani chikhululuko ndipo ndikulapa kwa Inu, ndipo madalitso a Allah atsitsidwe kwa Nabiy Jeete ndi banja lake lodalitsika.

4. Kapempheredwe ka ma rakaah atatu a Witr ndikuti udzayambe kuswali maraka awiri ndikupanga salaam. Pambuyo pake udzaimilira ndikuswalinso rakaah imodzi. Ngati wina atafuna atha kuswali marakah awiri ndikukhala tashahhud. Kenako adzaimirira ndikuswali raka yachitatu. Mnjira zonse ziwirizi, Qurutu idzawerengedwa mu rakaah yomaliza mutachoka pa rukuu. Mudzawerenga kaye Tahmiid yomwe ndi mawu onena Rabbanaa lakal hamdu ndipo kenako mudzawerenga Qunuut.

5. Imaam adzawerenga Qunuut mokweza. Munfarid adzawerenga mwakachetechete. Muqtadi adzanena kuti aameen momveka pambuyo pa mawu aliwonse a dua ya imaam mpaka imaam adzawerenge mawu onena kuti waqinii sharrah maa qadhwait. pambuyo pake, Muqtadi adzawerenga mawu omwewo omwe imaam amawerenga mpaka imaan atawerenga mawu okuti falakal hamdu ‘alaa maa qadhwait. Pambuyo pake muqtadi adzanenanso kuti aameen pambuyo pa mawu aliwonse mpaka kumapeto kwa dua.

Check Also

Allah akuonetsera chisangalalo chake pa Olemekezeka Maswahabah (radhwiyallahu anhum) a Mtumiki (swallallahu alaih wasallam)

Ndipo amene adatsogolera poyamba, ochokera m'gulu la ma Muhajirina ndi Answari, ndi omwe adawatsatira Iwo mwaubwino, Allah adzakondwa Nawo. Naonso adzakondwera Naye (pa Zomwe adzapatsidwe ndi Allah.) Ndipo wawakonzera minda yomwe mitsinje lkuyenda pansipake; adzakhala M'menemo muyaya. Uko ndikupambana Kwakukulu.