Cholengedwa chilichonse chimafunikira kudya kuti chipitilire kukhala ndi moyo, ndipo chakudya chili m’manja mwa Allah yekha.
Ziyenerezo, mphamvu ndi luntha sizizindikiro zodziwira umoyo wa munthu. Mawu a ndakatulo ndi oonadi:
ينال الفتى من عيشه وهو جاهل ويكدى الفتى في دهره وهو عالم
ولو كانت الأرزاق تجرى على الحجى هلكن إذا من جهلهن البهائم
Munthu amapeza chuma (chochuluka) ngakhale alibe nzeru. Munthu wina amasiyidwa ngati osauka, ngakhale kuti ali ndi maphunziro ndi luntha.
Kukadakhala kuti kagawidwe ka riziki kadakhanzikika pa nzeru, ndiye kuti nyamazo, chifukwa cha umbuli wawo, zikadaonongeka zonse.
Kudalira Allah Ta’ala
M’ Hadith yolemekezeka ya Mtumiki (swallallahu alaihibwasallam) Mtumiki swallallahu alaih wasallam adaulangiza Ummah kuti: “Ngati mutatsamira ndi kudalira Allah monga mukuyenerera kutero, Allah adzakupatsani mariziki monga momwe amazipatsira chakudya mbalame, Zimatuluka mu zisa zake m’mawa zili ndi njala, ndipo zimabwerera madzulo mimba zawo zitakhuta.”
Kupewa Haraam
Kudalira Allah ndiye chinsinsi chopezera kupambana pa moyo wa munthu komanso ndi njira yopezera barakah (madalitso) pa moyo wake. Komabe, kudalira Allah kumaphatikizaponso munthu kutsata njira za halaal kuti apeze zofunika pa moyo ndi kuonetsetsa kuti munthu asaphwanye malamulo a Allah nthawi ina iliyonse.
Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) adati: “E inu anthu! Opani Mulungu ndipo yesetsani kufunafuna riziki la Halaal. Ngati wina wa inu akuona kuti riziki lake lachedwetsedwa, asalifunefune m’njira yoti asamvere Mulungu chifukwa cha chisomo (barakah m’chuma) cha Allah sichingapezeke pochita machimo”.
Nkhani Ya Nabi Musah (‘alaihis salaam)
Zanenedwa kuti Nabii Musah atalandira uneneri ndikutumidwa ndi Allah kuti aitanire anthu ku Chisilamu, nkhawa ndi maganizo osamalira banja lake zidamufika m’mutu mwake.
Nthawi yomweyo, Allah adalamula Nabii Musah (alaihis salaam) kuti amenye thanthwe lina ndi ndodo yake. Atamenya thanthwelo, anapeza kuti thanthwelo linang’ambika, ndipo m’kati mwake munali mwala wina.
Nabii Musa pamenepa adalamulidwa kumenya thanthweli kachiwiri. Atalimenya, anapeza kuti mkati mwake munali mwala wachitatu.
Nabi Musah atamenyanso mwala wachitatu ndi ndodo yake, unang’ambika, ndikuonekera kachirombo kakang’ono komwe kamakhala mkati mwake. Kachilombo kakang’ono kameneka kanabisidwa mkati mwa miyala itatu, yobisika kwa anthu onse ndipo kankawoneka ngati sikali padziko lapansi, komabe kakudya chakudya chake chomwe Allah adakakonzera kwa iye Kenako Allah adamulora Nabii Musah (alaihis salaam) kuti amve mawu a kachilomboko omutamanda.
Kachilomboka kankamutamanda Allah m’mawu awa:
سبحان من يراني ويسمع كلامي ويعرف مكاني ويذكرني ولا ينساني
Ulemerero ukhale kwa Yemwe amandiona, ndi kumva zolankhula zanga, nadziwa kumene ndili ine, nandikumbukira, osandiiwala.
Nabii Musah alahis salaam atamva mawu a kachilombo oyamika Allah, adazindikira kuti Allah akufuna kumuwonetsa kuti Iye ndi Yemwe amapereka riziki kwa cholengedwa chilichonse ngakhale tizilombo tating’ono kwambiri, choncho Allah adzampezera zosoweka zake ndi banja lake.