Ntchito Yokondedwa Kwambiri Kwa Allah ndi Kuwerenga Qur’an mosalekeza
Ibnu Abbaas (radhwiyallahu anhuma) akusimba kuti munthu wina adamufunsa Rasulullah swallallahu alaihi wasallam kuti, “Kodi ndi ntchito iti yomwe ili yokondedwa kwambiri kwa Allah? Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) anayankha kuti, ‘Ntchito za halaal ndi murtahil (wapaulendo amene akaima paulendo wake, amayambiranso ulendo wake)’. Munthu uja adafunsa kuti, “E, Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) mkunena kuti kuchita zinthu za halaal ndi murtahil (wapaulendo amene waima paulendo wake kenako n’kuyamba ulendo wake), mukunena za ndani?” Mtumiki (Swallallaahu ´alayhi wasallam) adati: “Ine ndikunena za owerenga Qur’an Majiid yemwe (paulendo wake owerenga Buku la Allah amawerenga kuyambira koyambirira kwa Quraan mpaka kufika kumapeto, ndipo akafika kumapeto (kwa Quraan Majiid), kenako nkuyambanso (Qur’an Majeed). kuyambira pachiyambi)[1]
[1] سنن الترمذي، الرقم: 2948، وقال: هذا حديث غريب لا نعرفه من حديث ابن عباس إلا من هذا الوجه وإسناده ليس بالقوي، وقال الحاكم: له شاهد من حديث أبي هريرة، عن أبي هريرة رضي الله عنه قال: قام رجل إلى النبي صلى الله عليه وسلم فقال: يا رسول الله أي العمل أفضل أو أي العمل أحب إلى الله قال: الحال المرتحل الذي يفتح القرآن ويختمه صاحب القرآن يضرب من أوله إلى آخره ومن آخره إلى أوله كلما حل ارتحل (المستدرك على الصحيحين للحاكم، الرقم: 2090)