Ntchito yabwino yomwe Sa’d (radhiyallahu ‘anhu) adalandira nayo nkhani yabwino yokalowa Jannah

Olemekezeka Anas (radhwiya allaahu ‘anhu) anasimba kuti nthawi ina maSwahaabah (radhwiyallahu anhum) adakhala ndi Mtumiki (swalla allaahu ‘alayhi wasallam) pamene adati: “M’kanthawi kochepa aonekera munthu wa ku Jannah pamaso panu.” Nthawi yomweyo, Sa’d (radhwiyallahu anhu) adatulukira atanyamula nsapato zake kudzanja lake lamanzere, ndevu zake zikuchucha madzi a wudhu.

Tsiku lachiwiri ndi lachitatu, Mtumiki (swalla allaahu ‘alayhi wasallam) adalengezanso chimodzimodzi, ndipo masiku onse awiriwo munthu amene adalowa anali Sa’d (radhwiyallahu anhu).

Abdullah bun Amr bin Al-Aas (radhwiya allahu anhuma) adafuna kuti akakhale ndi Sa’d (radhwiya allahu anhu) kuti awone khalidwe lake ndi zochita zake kuti azindikire khalidwe lapadera kapena ntchito yomwe anali nayo chifukwa cha moyo wake zomwe zidachititsa kuti Mtumiki (swalla allaahu ‘alayhi wasallam) amuuze nkhani yabwino ya Jannah.

Choncho, tsiku lachitatu, Rasulullah (swalla allaahu alayhi wasallam) atachoka kumkunowo, Abdullah bin Amr (radhwiyallahu anhuma) anayimirira ndikumutsatira Sa’d (radhwiyallahu anhu) kuti alankhule naye. Atakumana naye Abdullah bin Amr (radhwiyallahu anhuma) adati kwa iye: “Ndasemphana maganizo ndi bambo anga, choncho ndalumbirira kuti sindibwerera kunyumba kwa masiku atatu? Ungandisungeko m’nyumba mwako kufikira atapita masiku atatu?”

Sa’d (radhwiyallah anhuma) adavomera ndipo Abdullah bin Amr (radhwiyallahu anhuma) adayamba kukhala naye. Komabe, ngakhale adali ndi chidwi chomuyang’anitsitsa m’masiku atatuwa Abdullah bin Amr (radhwiyallahu anhuma) sadaone chilichonse chomwe adachiona ngati chodabwitsa. M’malo mwake, sadamuoneko Sa’d (radhiyallahu anhul) akudzuka usiku kuti achite mapemphero a Tahajjud. Amangodzuka nthawi ya Fajr. maso ake ankayang’ana usiku ndipo ankatembenuka kuchoka mbali ina kupita mbali ina kama (bedi) lake, kuwerenga zikr asanagone.

Komabe, khalidwe lodziwika bwino lomwe Abdullah bin Amr (radhwiyallahu anhuma) adaliona mwa Sa’d (radhwiyallahu anhu) linali lakuti amangolankhula zabwino (zokhudza anthu ndipo ena, sadanenepo choipa chilichonse chokhudza aliyense).

Pambuyo pake masiku atatu atatha, ndipo Abdullah bin Amr (radhwiyallahu anhuma) sadaone zachilendo pamoyo wa Sa’d (radhwiyallahu anhu) chomwe chidachititsa apeze nkhani yabwino ya Jannah. Adaganiza zopita kwa Sa’d (radhwiyallahu ‘anhuma) ndikumufunsa kuti amuululire chifukwa chenicheni chomwe anafunira kukhala naye kwa masiku atatu.

Choncho, adapita kwa Abdullah (radhwiya allaahu ‘anhu) nati: “E, kapolo wa Allah! Kunena zoona, palibe kusagwirizana kapena kusemphana pa ubale wa pakati pa ine ndi bambo anga.

Koma chifukwa chimene ine ndimafunira kukhala nawe ndi chakuti kwa masiku atatu otsatizana, Mtumiki (swalla allaahu ‘alayhi wasallam) adalengeza motere: “Munthu wa ku Jannah watsala pang’ono kuonekera pa gulu lino”, ndipo pa masiku atatu onsewa ndiiwe munthu amene unaonekera. Ichi ndiye chifukwa chomwe ndinafunira kukhala nawe kuti ndione ntchito yabwino zako zabwino ndi makhalidwe ako ndi kutsanzira makhalidwe ako abwino. Koma (poona zochita zako) sindidapeze kuti Ukuchita zinthu zambiri za nafl, choncho ndiuze zabwino Zapadera zomwe umachita zomwe walandilira nkhani yabwino ya Jannah kuchokera kwa Mtumiki (swalla allaahu ‘alayhi wasallam)? “

Sa’d (radhwiya allaahu ‘anhu) adayankha: “Zomwe ndimachita ndi zomwe waonazo (Palibe chinanso m’moyo wanga chimene ndimachita kupatula zomwe wazionazi). Atamva izi Abdullah bin Amr (radhwiyallahu anhuma) adatembenuka kuti anyamuke. Koma pamene amatuluka, Sa’d (radhwiya allahu anhu) adamuitananso nati kwa iye: “Zomwe ndimachita ndi zimene waona. chifukwa chimene ine ndalandilira nkhani yabwino ya ku Jannah) ndikuti ine sindisunga mangawa mumtima mwanga a Msilamu aliyense, ndiponso sindikhala ndi nsanje mu mtima mwanga chifukwa cha ubwino uliwonse umene Allah Ta’ala wampatsa munthu wina.”

Atamva izi Abdullah bin Amr (radhwiyallahu anhuma) adati: “Iyi ndi ntchito yabwino yomwe yakupangitsa kuti ufike ulemelero wapamwamba uwu omwe waupeza, ndipo izi ndi zomwe ife (anthu) sitingathe kuchita pa moyo wathu.” (Musnad Ahmad #12807, Tareekh Dimashg 20/327, Musnadul Bazzaar #5836)

Check Also

Abu Ubaidah (Radhwiyallahu ‘anhu) aluza mano ake pa nkhondo ya Uhud

Pankhondo ya Uhud, Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) adamenyedwa koopsa ndi adani ndipo mano awiri …