19. Ngati mukufuna kusintha zobvala zanu m’chipinda chosungiramo Quraan Majiid, muyenera kuika kaye Qur’an Majiid m’kabati, m’dilowa ndi zina zotero musanavule. Kuvula pamaso pa Quraan Majiid ndikotsutsana ndi ulemu wa Quraan Majiid.
20.Ngati ukuwerenga ndime ya Sajdah kapena kuimvera ikuwerengedwa, zidzakhala Waajib (zokakamizidwa) kwa iwe kuchita Sajdah. Kapangidwe ka sajdah-e-tilaawat ndikuti umanena takbira ndi kupanga sajdah. kenako mudzanena takbira ndikunyamuka kuchoka pa sajdah. Ndi Mustahab kupanga sajdah kuchokera poima. Koma ngati izi zili zovuta, ndiye kuti n’zoloredwa kuchita sajdah utakhala.
Olemekezeka Abu Hurairah (radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) adati: “Mwana wa Adam akamawerenga ayat ya sajdah kenako nkuchita sajda, Satana amasuntha uku akulira nati:Kuonongeka kwa ine! Mwana wa Adam (alaihis salaam) adalamuridwa kupanga sajdah ndipo adapanga, choncho adzalandira Jannah. Ndidalamuridwa kupanga sajdah ndipo ndidakana, choncho ndidzalowetsedwa ku moto wa Jahannum.[1]
[1] صحيح مسلم، الرقم: 81