Olemekezeka Zubair (Radhwiya Allahu ‘anhu) Asolola Lupanga Lake Kuti Amutetezere Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam)

Olemekezeka Urwah bun Zubair (rahimahullah) akufotokoza motere

Nthawi ina yake, Shaitaan anafalitsa mphekesera yabodza yoti Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) wagwidwa ndi ma Kuffaar gawo la kumtunda kwa Makka Mukarramah. Atamva mphekesera imeneyi, Zubair (Radhwiyallahu ‘anhu), yemwe panthawiyo anali ndi zaka khumi ndi ziwiri zokha, nthawi yomweyo adanyamuka, nadutsa mchigulugulu cha anthu ndi lupanga lake pofunafuna Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam). Onse amene adamuona Zubair (Radhwiyallahu ‘anhu) ankadabwa nati: “Mwana wanyamula lupanga!” Atafika kwa Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam), Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) adamufunsa: “Kodi vuto ndi chiyani Zobuir? Zubair (radhwiya Allahu ‘anhu) adayankha pomudziwitsa Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) za mphekesera yabodza zonena kuti: zinafala nati, “Ndingathe kulimbana ndi amene akuika inu m’ mavuto ndi lupanga langa.”

Munkhani ina yomwe inalembedwa ndi mwana wa “Urwah (rahimahullah), Zubair (radhwiyallahu ‘anhu ndi munthu oyamba kusolola lupanga lake chifukwa cha Allah Ta’ala. Ndime iyi ikufotokozanso kuti pamene Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam). adamva yankho ili la Zubair (radhwiyallahu ‘anhu, adamupemphera ma du’a).

Zindikirani : Pali maganizo osiyana okhuza zaka za Zubair radhwiyallahu ‘anhu pa nthawi yomwe amavomereza chisilam. Pali malingaliro awiri osiyana omwe adanenedwa kuchokera kwa “Urwah (rahimahullah), Abul Aswad akusimba kuchokera kwa “Urwah (rahimahullah) kuti Zubair (radhwiyallahu ‘anhu) anali ndi zaka khumi ndi ziwiri pamene ankalowa chisilamu, ndipo Hishaam bin Urwah (rahimahullah) akusimba kuchokera kwa bambo ake, “Urwah (rahimahullah) kuti adali ndi zaka khumi ndi zisanu ndi chimodzi. Kunena za Hishaam bin ‘Urwah (rahimamillah), maganizo ake ndi oti Zubair (radhwiya Allahu ‘anhu) anali ndi zaka khumi ndi zisanu pamene ankalowa Chisilamu. Palinso maganizo ena onena kuti Zubair (radhwiyallahu ‘anhu) anali ndi zaka zisanu ndi zitatu pamene ankalowa Chisilamu. (Siyar A’laam min Nubaita 3/27, Uudul Ghaabak 2/210, Musand Abdur Razzang 19647, Musannaf ibn Abi Shaibah 1986)

Check Also

Ulemelero Wapamwamba wa Abu Ubaidah (Radhwiyallahu ‘anhu) Pamaso pa Abu Bakr (Radhwiyallahu ‘anhu)

Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) atamwalira, ma Ansaar adasonkhana ku Saqeefah Bitti Saa’idah …