Sunnah komanso miyambo yoyenera kutsatira usanayambe Kuwerenga Quraan Majiid 10

23. Ngati mudaloweza pamtima gawo lina lake la Qur’an Majiid, onetsetsani kuti mukulibwereza nthawi zonse kuti musaiwale. Hadith yachenjeza za kunyalanyaza kuwerenga Quraan ndi kuiwala zomwe waloweza pamtima.[1]

Olemekezeka Abu Musah Ash’ari (radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Rasulullah Adati: “Isamareni Qur’an Majiid. Ndikulumbirira Amene m’manja Mwake muli moyo wanga, (Qur’an Majiid) ikhoza kutuluka mwachangu kuchokera mu mtima kuposa momwe ngamira ingathawire pachingwe chake.”[2]

Olemekezeka Anas bun Maalik (radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Rasulullah Adati: “Mphotho za ntchito zabwino za Ummah wanga zinaonetsedwa kwa ine, mpaka (malipiro) a munthu yemwe wachotsa kachidutswa kakang’ono kamene kali mu nzikiti, komanso machimo a anthu a Ummah wanga zidaonetsedwa kwa ine, ndipo sindidaone tchimo lalikulu kuposa tchimo la munthu amene waiwala surah kapena Aayah ya Qur’an Majiid yomwe adadalitsidwa nayo.”[3]

Olemekezeka Ibnu Umar akufotokoza kuti Rasulullah (swallallahu alaihi wasallam) adati: “Fanizo la amene waloweza Qur’an pamtima lili ngati munthu omanga ngamira. Ngati apitiriza kuziyang’anira, zidzatetezeka, ndipo ngati angazisiye zomasura, zidzamuthawira.[4]

Olemekezeka Sa’d bun Ubaadah (radhwiyallahu anhu) akusimba kuti, Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) adati: “Palibe munthu amene amaphunzira Qur’an Majiid pambuyo pake ndikuiiwala, Kupatula kuti adzabwera pa tsiku la Qiyaamah ali wakhate.[5]

Zindikirani:

1. Mu Hadith imeneyi, tchimo loiwala Aayah kapena surah ya Quraan likulongosoledwa kuti ndi tchimo lalikulu kwambiri. Chifukwa chake ndi chakuti munthu akusonyeza kusathokoza kwa Allah pa ubwino waukulu umenewu wa Qur’an Majiid ponyalanyaza kuiwerenga ndi kuiwala zimene adadalitsidwa nazo.[6]

2. Ma Ulamaa ena afotokoza kuti chenjezo limene walongosoredwa mu Hadith imeneyi ndi wa amene amanyalanyaza kuwerenga Qur’an ndikuiwala zimene adaloweza.[7]

Ma Ulama enanso akuganiza kuti chenjezo ili ndi la amene amanyalanyaza kuwerenga Quraan Majiid kufikira kupatula kuiwala zomwe adaloweza amaiwalanso kuwerenga Quraan ndi maso.[8]


[1] وندب لحافظ القرآن أن يختم في كل أربعين يوما في كل يوم حزب وثلثا حزب أو أقل كذا في التبيين في مسائل شتى من ختم القرآن في السنة مرة لا يكون هاجرا كذا في القنية (الفتاوى الهندية 5/317)

[2] صحيح البخاري، الرقم: 5033

[3] سنن أبي داود، الرقم: 461، وقال العلامة النووي في روضة الطالبين 11/223: في إسناده ضعف وتكلم فيه الترمذي

[4] صحيح البخاري، الرقم: 5031

[5] سنن أبي داود، الرقم: 147، وقال العلامة العيني رحمه الله في شرحه على أبي داود 5/388: روى عن سعد بن عبادة وقيل عن رجل من خزاعة وروى عنه يزيد بن أبي زناد قال علي بن المديني: لم يرو عنه غيره وقال عبد الرحمن بن أبي حاتم عيسى بن فائد روى عمن سمع سعد بن عبادة فالحديث على هذا منقطع مع ضعفه

[6] وإنما قال: أوتيها دون حفظها إشعارا بأنها كانت نعمة جسيمة أولاها الله ليشكرها فلما نسيها فقد كفر تلك النعمة فبالنظر إلى هذا المعنى كان أعظم جرما وإن لم يعد من الكبائر واعترضه ابن حجر وقال: قول الشارح وإن لم يعد من الكبائر عجيب مع تصريح أئمتنا بأن نسيان شيء منه ولو حرفا بلا عذر كمرض وغيبة عقل كبيرة اهـ (مرقاة المفاتيح 2/605)

[7] فإن نسيان القرآن ليس أعظم الذنوب وإن عدَّه بعض العلماء من الكبائر كما نقله مولانا جلال الدواني عن الروياني في شرح العقائد العضدية لكن بعضهم أوّلوا بنسيانه بحيث لا يقدر على قراءته من المصحف والظاهر من الحديث نسيانها بمعنى عدم الحفظ عن ظهر القلب وعليه حمله الشارحون (لمعات التنقيح 2/475)

[8] إذا حفظ الإنسان القرآن ثم نسيه فإنه يأثم وتفسير النسيان أن لا يمكنه القراءة من المصحف (فتاوى الهندية 5/317)

Check Also

Ma Sunnah Komanso Miyambo Ya Dua 2

2. Popanga dua, kwezani manja anu mofanana ndi pachifuwa chanu (i.e. molingana ndi chifuwa chanu). …