Kutengapo mbali pa Nkhondo ya Badr

Ismaa’eel bin Abi Khaalid akuti Bahiyy (Rahimahullah) adati: “Panali anthu apakavalo awiri okha omwe ankamenyana ndi adani pa nkhondo ya Badr. Wina adali Olemekezeka Zubair (Radhwiyallahu ‘anhu) yemwe ankalimbana ndi adani kudzanja lamanja, ndipo winayo adali Miqdaad bun Aswad (Radhwiyallahu ‘anhu), yemwe ankamenya nkhondo kumanzere.

Hishaam bun Urwah akusimba kuti bambo ake Urwah (Rahimahullah) adati: “Zubair (Radhwiyallahu ‘anhu) adali atavala nduwira yachikasu tsiku la Badr. Jibreel (‘alaihis salaan) kenako adatsika ali ndi maonekedwe a Zubair (Radhwiyallahu ‘anhu). nayenso anali atavala nduwira yachikasu).”

Check Also

Kudziwa Kwambiri Dini kwa Muaaz bin Jabal (radhwiyallahu ‘anhu)

Abu Muslim Khowlaani (rahimahullah) akufotokoza kuti: “Ndinalowa mumzikiti wa Hims ndipo ndinaona gulu la anthu. …