binary comment

Dua

Dua ndi njira yomwe kapolo amadziyandikitsira nayo ku chuma chopanda malire cha Allah. Pali zabwino zambiri zomwe zanenedwa Mmahadith kwa amene amapanga dua. Rasulullah (Swallallahu alaihi wasallam) adanena kuti dua ndiye maziko a ibaadah zonse. Mu Hadith ina, Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adanena kuti Allah amakondwera ndi kapolo amene amapanga dua ndi kumupempha iye zofuna zake, ndipo Allah amakwiya ndi kapolo amene satembenukira kwa Iye ndi kumupempha zofuna zake. Kaŵirikaŵiri; padziko lapansi, anthu amakwiya ndi kutaya ulemu kwa munthu amene mosalekeza amafuna thandizo kwa iwo. Komabe, Allah, Mlengi wa chilengedwe chonse, ndi woti chikondi chake pa akapolo Ake chilibe malire. Choncho, Allah akulamula akapolo Ake kuti apitilize kutembenukira kwa Iye mu dua ndipo amakondwera nawo pamene akumpempha. Choncho, nkofunika kwambiri kwa msilamu kuipanga dua kukhala gawo la moyo wake wa tsiku ndi tsiku, kotero akuyenera kufunafuna chisomo cha Allah muzochita zake zonse ndi kufunafuna njira zothetsera mavuto ake onse.

Check Also

Ma Sunnah Komanso Miyambo Ya Dua 2

2. Popanga dua, kwezani manja anu mofanana ndi pachifuwa chanu (i.e. molingana ndi chifuwa chanu). …