M’mbuyomu Chisilamu chisanadze, Uthmaan bin Talhah anali oyang’anira makiyi a Ka’bah Shariif. Amatsegula Ka’bah Lolemba ndi Lachinayi, kuti anthu alowe ndikuchita ibaadah.
Nthawi ina, Hijrah isadachitike, pamene anthu ankalowa mu Ka’bah tsiku lawo lomwe adapatsidwa, Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) nayenso ankafuna kulowa. Komabe, Uthmaan bun Talhah sanamulore kuti alowe ndipo adamulankhula mwa mwano komanso mwaukali.
Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) moleza mtima adapirira kuzunzika kwake ndipo adamuuza kuti: “E, iwe Uthmaan! Likudza tsiku lomwe udzaona makiyi a Ka’ba ali m’manja mwanga, ndipo ndidzakhala ndi mphamvu zoipereka kwa iye aliyense amene ndikufuna.”
Uthmaan adayankha nati: “Tsiku limenelo lidzakhala loyalutsa kwa ma Quraishi! Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adati: “Ayi! Lidzakhala tsiku lolemekezeka kwa ma Quraishi.”
Uthmaan bin Talhah akunena kuti: “Ndidadziwa kuti ndithu tsikuli lidzafika, ndipo ndidali ndi chikhutiro chonse kuti zimene Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adanena ziyenera kuchitika.
Komabe idafika nthawi yomwe Allah adamulamula Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) ndi ma Swahaabah (Radhwiyallahu anhu) kuti asamukire ku Madina Munawwarah, ndipo nkhondo zambiri zowopsa zidachitika pakati pa Asilamu ndi ma Quraishi mzaka zomwe zidatsatiridwa.
Kenako idafika nthawi yomwe Allah adamemeza mtima wa Uthmaan bin Talhah kuti alowe Chisilamu. Choncho, adanyamuka kuchoka ku Makkah Mukarramah kupita ku Madina Munawwarah m’chaka cha 7 pambuyo pa nsamuko kuti akalengeze za kulowa chisilamu kwake ndi lonjezo lake lovomereza chisilamu pamaso pa Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam).
Patadutsa chaka chimodzi, nthawi ya Fath-e-Makkah (kugonjetsa Makka), Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adamulangiza Uthmaan bin Talhah (Radhwiyallahu anhu) kuti abweretse makiyi a Ka’aba popeza makiyi a Ka’aba ankasungidwa ndi banja limeneli.
Atabweretsa makiyiwo, Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adalowa m’gawo la Ka’bah ndikuchita ibaadah. Pambuyo pake, Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) atatulukamo, Abbaas ndi Ali (Radhwiyallahu anhuma) onse ankafuna kuti apatsidwe ulemu okhala adindo a makiyi a Ka’bah Shariif.
Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) ali mu Ka’bah, Allah adavumbulutsa ayah ya Qur’an, kumulangiza kuti abweze dalitso kwa Uthmaan bun Talhah (Radhwiyallahu anhu) ndi akubanja kwake.
Allah Ta’ala adati:
إِنَّ اللَّهَ يَأْمُرُكُمْ أَن تُؤَدُّوا الْأَمنتِ إِلَىٰ أَهْلِهَا
Ndithu Allah akukulamurani kuti mubwezere zomwe mwakhulupirika nazo kwa eni ake.
Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) kenaka adabweza makiyi kwa Uthmaan bin Talhah (Radhwiyallahu anhu) namuuza kuti makiyi adzakhala m’manja mwa akubanja kwake ndipo palibe amene adzatenge kuchokera kwa iwo kupatula opondereza.
Uthmaan bin Talhah (Radhwiyallahu anhu) akuchoka ndi makiyi, Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adamuitana nati: “E Uthmaan! Kodi ukukumbukira mawu omwe ndidakuuza m’mbuyomu kuti posachedwa tsiku likubwera pomwe udzaona makiyi a Ka’aba ali m’manja mwanga, ndipo ndidzakhala ndi mphamvu zowapereka kwa aliyense amene ndikufuna?”
Uthmaan bun Talhah (Radhwiyallahu anhu) anayankha: “Inde, Mtumiki wa Allah (Swallallahu alaihi wasallam)! ndikulikumbukira tsiku limenelo!”
Kuchokera m’ndime yomwe yatchulidwa pamwambayi ya Qur’an Majiid, tikuphunzira kuti zosungitsidwa zonse ziyenera kubwezedwa kwa amene ali oyenera. M’mahadith, Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wasallam) watsindika kwambiri pakukwaniritsa ma lonjezo.
Munthu Aliyense Ali Ndi Udindo Okwaniritsa ntchito yake
Ziyenera kumveka bwino kuti kukhulupirika pa Amaanah (kuyang’anira bwino ntchito yomwe wapatsidwa) sikunagone pa chuma pokha chomwe wasungitsidwa ndi munthu, koma kumaphatikizapo udindo ulionse (kaya wadziko kapena dini) umene wapatsidwa.
Imaam wa mzikiti, muazzin, mutawalli (oyang’anira musjid kapena gulu la chisilamu), olamulira kapena otsatira, mphunzitsi kapena ophunzira, olemba ntchito kapena wantchito, ogula kapena ogulitsa, mwamuna kapena mkazi, makolo. kapena ana, okhala nawo pafupi kapena Othandizana nawo onse apatsidwa udindo umene ali nawo kuchokera kwa Allah ndi zolengedwa. Popeza, Udindo waukulu omwe munthu angapatsidwe ndiye ndi udindo okhudza za Dini.
Tipemphe Allah kuti atidalitse ndi tawfiiq (kuthekera) yokwaniritsa udindowu molondora ndi motsatira malamulo a shari’ah.