Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam) Kusankha Abdur Rahmaan bin Auf (radhwiya Allahu ‘anhu) kukhala Mtsogoleri wa Asilikali pa nkhondo ya Dumatul Jandal.

M’chaka cha chisanu ndi chimodzi chioangireni Hijrah, m’mwezi wa Sha’baan, Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) adalankhula ndi Abdur Rahmaan bin Auf (Radhwiyallahu ‘anhu) nati kwa iye: “Konzekeretsa ulendo wako, popeza ndikufuna ndikutumize ku ulendo, mwina lero kapena mawa, Insha Allah.

M’mawa mwake, Abdur Rahmaan bun Auf (Radhiyallahu ‘anhu) adabwera pamaso pa Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam), atavala nduwira yakuda. Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) adamasula nduwira yake ndikuimanga pamutu pake, mchira ukulendewera kumbuyo kwake. Utali wa mchirawo unali pafupifupi utali wa zala zinayi. Kenako Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) adati kwa iye: “E, iwe Ibnu Auf! Umu ndi momwe uzimsngira nduwira yako pooeza ndiye mchitidwe wa ma Arab omwenso ndi wabwino kwambiri.

Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam) adasankha Abdur Rahmaan bin Auf (Radhwiyallahu ‘anhu) kukhala mtsogoleri wa gulu lankhondo choncho adamuuza Bilaal (Radhwiyallahu ‘anhu) kuti amupatse mbenderayo. Kenako Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) adamtamanda Allah Ta’ala, natumiza malonje kwa iye mwini, nati:

“E, iwe Ibnu Auf! Tenga mbendera, ndipo nyamukani panjira ya Allah pamodzi ndi gulu lankhondo. Kalimbaneni ndi anthu amene Sakhulupirira Allah Taala. Musabe zolandidwa pankhondo, Osatsutsana ndi malonjezano anu (omwe mudapangana ndi adani), Osadula matupi a adani, ndipo musaphe ana. Ili ndi lamulo la Allah Ta’ala lomwenso ndi njira Mtumiki wake yemwe anadza kwa inu.”

Pambuyo pake, Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) adamtumiza iye panjira ya Allah Ta’ala pamodzi ndi gulu lankhondo ya anthu mazana asanu ndi awiri kupita ku fuko la Kalb, lomwe lili pamalo otchedwa Dumat al-Jandal. Kenako Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) adamulangiza motere:

“Ngati anthu a pamalopo avomereza (Chisilamu), ukwatire mwana wamkazi wa mtsogoleri wawo.

Choncho Abdur Rahmaan (Radhwiyallahu ‘anhu) adanyamuka ndi asilikali ake mpaka kukafika kwa anthu a ku Dumat al-Jandal. Anakhala kumeneko masiku atatu, akuwaitanira ku Chisilamu.

Pa tsiku lachitatu, mtsogoleri wa Dumat al-Jandal, Asbagh, yemwe anali Mkhristu, adavomera Chisilamu. Anthu ena ambiri a fuko lake adavomerezanso Chisilamu. Amene adasankha kusavomereza Chisilamu adavomereza kupereka jizyah.

Kenako Abdur Rahmaan (Radhwiya Allaahu ‘anhu) adalembera kalata Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) kumudziwitsa zomwe zidachitika ndikumutsimikiziranso ngati akwatire mwana wa mtsogoleri wawo. Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) adayankha kalata yake yoti apitilire ndi maganizo okwatira mwana wa mtsogoleri, Asbagh. Choncho Abdur Rahmaan (Radhwiyallahu ‘anhu) anakwatira mwana wake wamkazi dzina lake Tumaadhir (radhwiyallahu ‘anha). (Bazzaar #6175, Majma’uz Zawaaid #9615, Sharhuz Zurqaani 3/133)

Check Also

Abdur-Rahman bin Awf (Radhwiyallahu ‘anhu) amatsogolera Swalaah

Paulendo wa Tabuuk, ma Swahaabah (Radhwiyallahu ‘anhum) adali pa ulendo ndi Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi …