Pamene Allah Ta’ala ankamulamula Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) kuti anyamuke ulendo wa ku Tabuk, ma Swahaabah ambiri adalibe kalikonse panthawiyo zoti athandizikirw kuyende ulendo wautali ndi wotopetsa, makamaka pamene ankayembekezera kukumana ndi gulu lankhondo lachiroma pankhondo yomwe inali ndi zida zokwanira komanso adalipo ambiri.
Choncho pofuna kusonkhanitsa pamodzi ndi kukonzekeretsa asilikali, Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) adawalimbikitsa ma Swahaabah (Radhwiyallahu ‘anhum) kuti apereke chuma mnjira ya Allah Ta’ala. Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) adawalimbikitsa kuti athandize amene adalibe zowayenereza kupita nawo ku ulendowo ndipo adawalonjeza kuti m’malo mwa chithandizochi, adzalandira malipiro aakulu kwa Allah Ta’ala. Mwanjira imeneyi, ma Swahaabah ambiri osauka (Radhwiyallahu ‘anhum) adapatsidwa katundu ndi zida zapaulendo.
Abdullah bin Abbaas (Radhwiya Allaahu ‘anhuma) adati:
Nthawi imeneyo, mwa ma Swahaabah amene anapereka chuma chochuluka anali Abdur Rahmaan bin Auf (Radhwiyallahu ‘anhu). Adapereka Uqiyah mazana awiri (200) asiliva (ndalama zasiliva zikwi zisanu ndi zitatu (3000)).
Pa nthawiyo, Umar (Radhwiyallahu ‘anhu) anati: “E, Mtumiki wa Allah (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam)! Ndikuganiza kuti Abdur Rahmaan (Radhwiyallahu ‘anhu) sanasiye kalikonse ku banja lake.’
Kenako Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) adalankhulandi Abdur Rahmaan bun Auf (Radhwiya Allaahu ‘anhu) namufunsa: “Kodi wasiya chilichonse kubanja lako?”
Adayankha, “Inde, ndawasiira zambiri kuposa zomwe ndapereka, ndipo zomwe ndidawasiyira nzabwino kwa iwo.”
Kenako Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) adamufunsa: ‘Kodi mwawasiira zingati?” Iye anayankha kuti: ‘Ndinawasiyira malonjezo a Allah Ta’ala ndi Mtumiki Wake (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) oti adzalandira zabwino ndi mariziki (popereka nsembe chifukwa cha Din).
Kuchokera pankhaniyi, tikuona kuti Abdur Rahmaan bun Auf (Radhiyallahu ‘anhu) ndi banja lake adapereka chuma chonse chomwe adali nacho pa nthawiyo chifukwa cha Allah Ta’ala. (Taarikh Ibn Asaakir 2/28)