Sayyiduna ‘Abdur Rahmaan bin ‘Auf (Radhiyallahu ‘anhu) apatsidwa Udindo osankha Khalifah.

Pambuyo pake, Sayyiduna “Umar (radhiyallahu ‘anhu) adapanga Shura (gulu la akuluakulu omwe azipanga ziganizo) lokhala ndi ma Swahaabah asanu ndi mmodzi otsatirawa: Ali (radhiyallahu ‘anhu), ‘Uthmaan (radhiyallahu ‘anhu), Zubair (radhiyah ‘anhu) Sa’d (Radhiyallahu ‘anhu) ndi Abdur Rahmaan bun ‘Auf (radhiyallahu ‘anhu).

Pankhani ya ma Sahaabah asanu ndi mmodziwa (Radhiyallahu ‘anhum), Umar (Radhiyallahu ‘anhu) adanena kuti: “Sindikupeza kuti anthu ali oyenera kutsata Khilaafah kuposa gulu ili la maSwahaabah (Radhiyallahu ‘anhum) chifukwa chakuti Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) adawasiya ali ndi moyo wosangalala padziko lapansi.”

Pamene Umar (Radhiyallahu ‘anhu) adamwalira, Miqdaad bun Aswad (Radhiyallahu ‘anhu) adasonkhanitsa anthu a Shura m’nyumba ya Miswar bun Makhramah (radhiyallahu ‘anhu). Kenako adakhala mashyra kuti achite chigamulo pomwe Abu Talhah (Radhiyallahu ‘anhu) adayimilira kuletsa anthu kulowa ndi kusokoneza Shura.

Anthu a m’Shura adagwirizana kuti atatu aiwo asiya ufulu wawo ndikuupereka kwa ena omwe ali m’Shura. Mwanjira imeneyi, Zubair (radhiya Allahu ‘anhu) adapereka ufulu wake kwa Ali (radhiyallahu ‘anhu), Sa’d (radhiyallahu ‘anhu) adapereka ufulu wake kwa Abdur Rahmaan bin ‘Auf (radhiyallahu ‘anhu), ndipo Talhah adasankha ‘Ufulu wake’ kw Uthman (Radhiyallahu ‘anhu).

Nayenso Abdur Rahmaan bun ‘Auf (Radhiyallahu ‘anhu) adavomera kusiya ufulu wake wa khilaafah pokhapokha ataloredwa kusankha kuti ndi ndani mwa awiriwa amene asankhidwe kukhala Khalifa. ‘Uthmaan (Radhiyallahu ‘anhu) ndi Ali (Radhiyallahu ‘anhu) adagwirizana ndi ganizo lake ndipo adalonjeza kuti atsatira ndi mtima onse chisankho chake. Kenako mamembala a Shura adabalalika.

Kwa masiku atatu ndi mausiku atatu otsatira, Abdur Rahmaan bin ‘Auf (Radhiyallahu ‘anhu) adapita kwa anthu a mumzinda wa Madinah Munawwarah, kuwafunsa kuti ndi ndani amene akuona kuti ayenera kusankhidwa kukhala Khalifa.

Abdur Rahmaan bin ‘Auf (Radhiyallahu ‘anhu) sanagone movutikira m’masiku atatu ndi mausiku amenewa. M’malo mwake, ankapitiriza kuswali, du’aa, istikhaarah ndi kufunsa anthu.

Patatha masiku atatu usana ndi usiku, Abdur Rahmaan bun ‘Auf (radhiyallahu ‘anhu) anadza kwa mphwake Miswar bun Makhramah (radhiyallahu ‘anhu). Pofika. anampeza ali mtulo, namudzutsa iye nanena. “Iwe Miswar ukugona?

Kenako Abdur Rahmaan (Radhiyallahu ‘anhu) adamuuza kuti: “Pita ukamuitane Ali (Radhiyallahu ‘anhu) ndi ‘Uthmaan (Radhiyallahu ‘anhu).” Hazrat Miswar (Radhiya Allahu ‘anhu) adafunsa kuti: “Ndiyambe ndindani kumuitana?” Abdur Rahmaan (Radhiyallahu anhu) adayankha: “Amene wamfuna.”

Kenako Miswar (Radhiyallahu ‘anhu) adapita kwa Ali (radhiyallahu ‘anhu) ndi “Uthmaan (radhiyallahu ‘anhu) akuwauza kuti Hazrat Abdur Rahmaan (Radhiyallahu ‘anhu) akuwaitana. Choncho atatuwa adanyamuka ulendo opita kwa ‘Abu Hurahiyah.

Atafika kunyumba ya Miswar (Radhiyallahu ‘anhu), adampeza Abdur Rahmaan bin ‘Auf (radhiyallahu ‘anhu) ali chiyimire kuswali. Atamaliza Swalah yake adatembenukira kwa ‘Ali (Radhiya Allaahu ‘anhu) ndi ‘Uthmaan (Radhiyallahu ‘anhu) nati: “Ndidawafunsa anthu za inu nonse awiri, ndipo sindinapezepo wina aliyense kukhaka opambana pa udindo kuposa awirinu.” Abdur Rahman Radhiyallah anhu adapanga Hazrat Ali (Radhiyallahu ‘anhu) ndi Hazrat ‘Uthmaan (Radhiyallahu ‘anhu) alonjeza kuti mwa awiriwa, yemwe angamusankhe kukhala Khalifa ndithu adzalamulira mwachilungamo, ndipo amene sasankhidwa adzakondwera ndi chigamulo chomwe chingapangidwe ndikuvomera munthu wina kukhala Khalifa.

Hazrat Abdur Rahmaan (Radhiya Allaahu ‘anhu) pambuyo pake adavala nduwira yomwe Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) adamumanga mutu mwake, adakolekera lupanga lake ndikupita ndi Hazrat Ali (radhiyallahu ‘anhu) ndi Hazrat ‘Uthmaan (radhiyallahu ‘anhu) kupita ku musjid. Hazrat Abdur Rahmaan (Radhiyallahu ‘anhu) adatumiza uthenga owayitanira anthu ku Musjid. Choncho, anthu anayamba kusonkhana musjid, kupanga mizere, mpaka musjid idadzadza ndi anthu.

Hazrat ‘Uthmaan (Radhiya Allaahu ‘anhu) sadathe kupeza malo aliwonse oti akhale choncho chifukwa cha kuchuluka kwake kwa hayaa (kudzichepetsa kwake), adakhala kumbuyo kwa anthu onse mu musjid.

Kenako Hazrat Abdur Rahmaan (Radhiya Allaahu ‘anhu) adakwera pa mimbar ya Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam) naima pa malo omwe Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam) ankakhalapo. Adayima pamenepo kwa nthawi yayitali ndikupanga mokweza mawu. Kenako adayankhula kwa anthu kuti: “E inu anthu! Ine ndakufunsani (za Hazrat Ali (Radhiyallahu ‘anhu) ndi Hazrat ‘Uthmaan (Radhiyallahu ‘anhu)) mwamseri ndi pagulu, awiriawiri ndi payekhapayekha, ndipo ndapeza kuti simunafanane aliyense mwa inu ndi ma Swahaaba awiriwa.”

Kenako Hazrat Abdur Rahmaan (Radhiya Allaahu ‘anhu) adagwira dzanja la Hazrat “Uthmaan (Radhiyallahu ‘arihu) namulengeza kuti ndiye akhale Khalifah, kenako adamukhanzika Hazrat “Uthmaan (Radhiyallahu anhu) pa sitepe ya mimbari yomwe ili pansi pake kuti anthu abwere kwa iye ndi kugwirana naye dzanja kulonjeza kuti adzamumvera. Kuchokera mwa anthu onse, Hazrat Ali (Radhiyallahu ‘anhu) ndi amene adayamba kubwera ndikulonjeza kuti adzakhala okhulupirika kwa Hazrat ‘Uthmaan (Radhiyallahu ‘anhu). (Al-Bidaayah-wan-Nihaayah vol 7 tsamba 297-298)

Check Also

Olemekezeka Abu Zar (Radhwiyallahu ‘anhu) Kulemekeza Alendo

‘Isa bin ‘Umailah (Rahimahullah) akufotokoza za munthu wina amene adawona khalidwe la Abu Zar (Radhwiyallahu …