Ma Sunnah Komanso Miyambo Yokaonera Odwala

1. Ndi mustahab (zofunika kwambiri) kupanga wudhu usanakamuyendere odwala.[1]

Olemekezeka Anas Radhwiyallahu anhu akusimba kuti Rasulullah swallallahu alaihi wasallam adati; “Amene wapanga wudhu wangwiro (pokwaniritsa masunnah ndi ma mustahab onse a wudhu) ndi kupita kukacheza ndi m’bale wake wachisilamu yemwe akudwala ndi chiyembekezo cholandira malipiro oyendera odwala, munthu oteroyo adzaikidwa kutali ndi Jahannum kwa ntunda wa zaka makumi asanu ndi awiri (70,000).[2]

2. Koyendera odwala, musatalikitse nthawi yomuchezetsa, kuteroko kutha kuchititsa odwala kukudandaurani. M’malo mwake, muyenera kuchoka pakapita kanthawi kochepa.[3]

Kwanenedwanso kuti Ibnu Abbaas Radhwiyallahu anhuma adati: “Zikuchokera ku masunnah kufupikitsa nthawi yokhala ku ulendo (omwe mwakacheza ndi odwala) ndi kupewa kuchita phokoso.[4]

3. Mulimbikitseni odwala ndi kumupatsa chiyembekezo chakuti achira. Kuli kosayenera kuti dokotala kapena munthu aliyense auze odwalayo kuti palibe chiyembekezo chirichonse kwa iye pathandizo lirilonse.

Olemekezeka Abu Sa’eed Khudri adanenanso kuti Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adati: “Mukamchezera munthu odwala, mupatseni chirimbikitso ndi chiyembekezo chokhala ndi moyo, pakuti ndithu kumpatsa chiyembekezo sikumasintha chikonzero cha Allah, idzakhala njira yobweretsera chisangalalo ndi chitonthozo kwa iye.”[4]

Olemekezeka Ibnu Abbaas Radhwiyallahu anhuma akufotokoza kuti Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) nthawi ina adayendera odwala yemwe adali wakumudzi, ndipo akamayendera odwala, ankawerenga duwa iyi mobwerezabwereza:

لا بَأْسَ طَهُورٌ إِنْ شَاءَ اللهُ

Palibe chifukwa chodera nkhawa, kudzera mu matendawa, muyeretsedwa insha-Allah.[5]


[1] من عاد متوضيًا ويكون فائدة الوضوء أنه ربما يطلب المريض الدعاء منه فيدعو له، وعلى الثاني فينبغي أن يكون الوضوء مستحبًا للعيادة (فتح الودود في شرح سنن أبي داود 3/ 384)

(عن أنس بن مالك قال: قال رسول الله – صلى الله عليه وسلم -: من توضأ فأحسن الوضوء) أي: أسبغه (4) وأتمه، أو أتى بآدابه وسننه، وفيه استحباب العيادة على وضوء شرح سنن أبي داود لابن رسلان 13/ 288)

[2] سنن أبي داود، الرقم: 3097، سكت عنه الحافظ في الفصل الثاني من هداية الرواة (2/163) وقد قال في مقدمته (1/58): وما سكت عن بيانه فهو حسن

[3] مرقاة المفاتيح 3/1153

[4] سنن الترمذي، الرقم: 2087، وقال هذا حديث غريب

[5] صحيح البخاري، الرقم: 5656

Check Also

Ma Sunnah Komanso Miyambo Ya Jumu’ah 1

1. Werengani Surah Dukhaan Lachinayi usiku. Olemekezeka Abu Hurairah (radhwiyallah anhu) akunena kuti Rasulullah (swallallahu …