4. Mukamayendera odwala, pemphani dua iyi:
لا بَأْسَ طَهُورٌ إِنْ شَاءَ اللهُ
Palibe chifukwa chodera nkhawa, insha-Allah kudzera mu matendawa, muyeretsedwa.
Mukhozanso kubwereza dua iyi kasanu ndi kawiri:
أَسْأَلُ اللهَ الْعَظِيمَ رَبَّ الْعَرْشِ الْعَظِيمِ أَنْ يُشْفِيكَ
Ndikumupempha Allah Wamphamvu zoposa, Mbuye wa Mpando Wachifumu waukulu, kuti akuchizeni.
عن ابن عباس عن النبي صلى الله عليه وسلم قال: من عاد مريضا لم يحضر أجله فقال عنده سبع مرار: أسأل الله العظيم رب العرش العظيم أن يشفيك إلا عافاه الله من ذلك المرض (سنن أبي داود، الرقم: 3106، سنن الترمذي، الرقم: 2083، وقال: هذا حديث حسن غريب لا نعرفه إلا من حديث المنهال بن عمرو)
Olemekezeka Ibnu Abbaas Radhwiyallahu anhuma akufotokoza kuti Rasulullah swallallahu alaihi wasallam adanena kuti amene angawerenge duwa yomwe yatchulidwa pamwambayi kasanu ndi kawiri kwa munthu odwala yemwe sadayenera kufa ndi matendawo, Allah amuchiritsa ku matendawo.
5. Ngati sizingabweretse vuto kwa odwala, Mpempheni kuti akupangireni dua.
عن عمر بن الخطاب قال: قال لي النبي صلى الله عليه وسلم: إذا دخلت على مريض، فمره أن يدعو لك فإن دعاءه كدعاء الملائكة (سنن ابن ماجة، الرقم: 1441، وإسناده حسن كما في مسند الفاروق لابن كثير 1/228)
Olemekezeka Umar Radhwiyallahu anhu akusimba kuti Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adati: “Pamene mwakamuyendera odwala (ngati kuli kotheka kumupempha kuti akupangireni dua) mpempheni kuti akupemphereni kwa Allah. ndithu, duwa yake ili ngati duwa ya angero (chifukwa choyeretsedwa kumachimo ake).
6. Sunnah yoyendera odwala siili kwa achibale ake kapena abwenzi ake okha. Ngati munthu akudziwa za Msilamu amene akudwala, ndipo nkotheka kuti apite kukamuona, achite zimenezo.
Zindikirani: Zanenedwa kuti Rasulullah Swallallahu alaihi wasallam adayendera mwana wachiyuda yemwe ankadwala, ndipo Rasulullah Swallallahu alaihi wasallam adamuitanira ku Chisilamu ndipo Mwanayo adalowa Chisilamu kenako ndikumamwalira.
Choncho, Ma Ulama akufotokoza kuti kafiri akadwala nkoloredwa kukamuona. Munthu akamakamuyendera azipanga Niya yomuitanira ku Chisilamu.
Kuyenera kukumbukiridwa kuti kuyendera kaafir kudzaloredwa pokhapokha ngati munthu watsimikiza kuti sadzaika pachiswe Dini yake mwanjira iliyonse. Choncho, ngati pali china chotsutsana ndi Chisilamu (monga kupezeka kwa ntanda m’nyumbamo, kuyimba nyimbo, kusakanikirana kwa amuna ndi akazi omwe si apachibale, ku9ezeka kwa zithunzi kapena mafano, ndi zina zotero) m’zochitika zonsezi sikudzaloredwa kwa munthu kuyendera. ndi Kaafir.
Alislaam Yeretsani mtima wanu potsatira chisilamu