
Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) adati: “Ndithu, amene angadzasamalire akazi anga ndikadzamwalira, ndiye munthu owona ndi owopa Allah.
Atamwalira Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam), Olemekezeka Abdur Rahmaan bun Auf (Radhwiyallahu ‘anhu) ankakhala myandikana ndi Azwaaj Mutahharaat (akazi olemekezeka a Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam)). Momwemonso akayamba ulendo wa Haji, Olemekezeka Abdur Rahmaan ndi Olemekezeka Uthmaan (Radhwiyallahu ‘anhuma) ankayesetsa kukaonetsetsa kuti Azwaaj Mutahharaat akhale omasuka.
Asadanyamuke Oleme Abdur Rahmaan (Radhwiyallahu ‘anhu) amakonzekera zokwera zomwe zigwiritsidwe ntchito ndi Azwaaj Mutahharaat. Ankaika nsalu zikuluzikulu zobiriwira pamwamba pa zokwerazo (chifukwa cha ulemu ndi kuwalemekeza Azwaaj Mutahharaat).
Uthmaan (Radhwiya Allaahu ‘anhu) ankalengeza (kwa alendo ena) kuti munthu asayandikire pafupi ndi ngolo kapena kuyang’ana m’menemo.
Uthmaan (Radhwiyallahu ‘anhu) ankayenda kutsogolo kwa nyama zomwe zinaikidwapo ngolo za Azwaaj Mutahharaat (Radhwiyallahu ‘anhun) ndi Sayyiduna Abdur Rahmaan bin Auf (Radhwiyallahu ‘anhu) ankayenda kumbuyo kwake. Akayandikira mwamuna, nthawi yomweyo ankamuuza iye: “Choka pangolopa!
Paulendowu, gulu la apaulendo likaima malo alionse, Sayyiduna Abdur Rahmaan (Radhwiyallahu ‘anhu) ndi Uthmaan (Radhwiyallahu ‘anhu) ankaonetsetsa kuti nyama zonyamula Azwaaj Mutahharaat (Radhwiyallahu ‘anhun) ziime patali ndi chigwacho. Abdur Rahmaan bun Auf komanso Uthmaan (Radhwiyallahu ‘anhuma) ankamanga msasa kumapeto kwa chigwacho (kuteteza Azwaaj Mutahharaat ndi kuonetsetsa kuti palibe mwamuna oyandikira kwa iwo). (Fathul Baari 4/73, At-Tabaqaatul Kubra 8/169, Fadhaailus Sahaabah Li Ahmad bin Hambal #1252)
Alislaam Yeretsani mtima wanu potsatira chisilamu