Dua Yoyamba
لا يَأْسَ طَهُورٌ إِنْ شَاءَ الله
Palibe chifukwa chodera nkhawa, insha-Allah kudzera m’matendawa, muyeretsedwa. (i.e. Palibenso chifukwa chilichonse choti mude nkhawa kapena kuchita mantha. Mukungoyeretsedwa ku Uzimu, mukuyeretsedwa ku machimo anu, ndipo kuthupi, thupi lanu likuyeretsedwa ku poizoni. Choncho, pamene matenda abwera kwa inu ngati chifundo chobisika kumbali ya Allah palibe chifukwa chodandaulira ndi kukhumudwa.[1]
Dua Yachiwiri
Werengani dua iyi kasanu ndi kawiri:
أَسْأَلُ اللهَ الْعَظِيمَ رَبَّ الْعَرْشِ الْعَظِيمِ أَنْ يُشْفِيَكَ
Ndikupempha Allah Wamphamvu zoposa, Mbuye wa Mpando Wachifumu waukulu, kuti akuchizeni.
عن ابن عباس عن النبي صلى الله عليه وسلم قال: من عاد مريضا لم يحضر أجله فقال عنده سبع مرار: أسأل الله العظيم رب العرش العظيم أن يشفيك إلا عافاه الله من ذلك المرض(سنن أبي داود، الرقم: 3106، سنن الترمذي، الرقم: 2083، وقال: هذا حديث حسن غريب لا نعرفه إلا من حديث المنهال بن عمرو)
Olemekezeka Ibnu Abbaas Radhwiyallahu anhu akusimba kuti Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) adati: “Amene angamuwerengere duwa iyi kasanu ndi kawiri munthu akudwala yemwe sadayenera kumwalira ndi matendawo, Allah adzamuchiritsa ku matendawo.
أَسْأَلُ اللهَ الْعَظِيمَ رَبَّ الْعَرْشِ الْعَظِيمِ أَنْ يُشْفِيَكَ
Duwa Yachitatu
أَذْهِبِ الْبَأْسَ رَبَّ النَّاسِ وَاشْفِ أَنْتَ الشَّافِي لَا شِفَاءَ إِلَّا شِفَاؤُكَ شِفَاءَ لَا يُغَادِرُ سَقَمًا
Chotsani masautso, E Mbuye wa anthu onse, ndipo perekani machiritso.[3]
Dua Yachinayi
باسْمِ اللهِ أَرْقِيكَ مِنْ كُلِّ شَيْءٍ يُؤْذِبْكَ مِنْ شَرِّ كُلِّ نَفْسٍ أَوْ عَيْنٍ حَاسِبْكَ مِنْ شَرِّ كُلِّ نَفْسٍ أَوْ عَيْنٍ حَاسِبْدَ بِاسْمِ اللهِ أَرْقِبْكَ
M’dzina la Allah Ndikukuwerengerani (mawu awa) Ndikupempha chithandizo kwa Allah pa Chilichonse chimene chikupezeni choipa kuchokera ku mzimu uliwonse (oipa) kapena diso ladumbo. Allah akupatseni machiritso. M’dzina la Allah Taala Ndakuwerengerani.[4]
[1] صحيح البخاري، الرقم: 5656
[2] صحيح البخاري، الرقم: 5750
[3] صحيح مسلم، الرقم: 2186