Ana Olungama – Cholowa Cha Tsiku Lachiweluzo

Zina mwa zabwino zamtengo wapatali za Allah pa munthu ndi mdalitso okhala ndi ana. Mdalitso okhala ndi ana ndi ena mwa Ni’ma yapadera ya Allah, zomwe zatchuridwa mu Quraan Majiid. Allah  Akunena:

وَاللَّهُ جَعَلَ لَكُم مِّنْ أَنفُسِكُمْ أَزْوَاجًا وَجَعَلَ لَكُم مِّنْ أَزْوَاجِكُم بَنِينَ وَحَفَدَةً وَرَزَقَكُم مِّنَ الطَّيِّبَاتِ

Allah adakulengerani akazi a mtundu wanu, ndipo adakupangirani ana ndi zidzukulu kuchokera mwa Akazi anuwo, ndipo adakupatsani zinthu zabwinozabwino.

Mitendere yambiri ya Allah ndiyoti phindu ndi ubwino wake zimakhala pa moyo wa munthu. Komabe, mphatso ya ana ndiye mpamba omwe siumangochulukira ubwino wake pa munthuyo pamene ali moyo pokha, komanso zimapitiriza kumupindulira ngakhale akamwalira.

Komabe, mpambawu umampezetsa zabwino munthu ngati ataikamo makhalidwe a Dini mwa ana ake ndi kuwalumikiza kwa Allah. Mpaka pamene ana ake angasamaritse Dini m’moyo mwawo ndi kutsata ziphunzitso chake chomwe iye amawaphunzitsa. kwa iwo, ndalama zake zidzapitiriza kumpezera zabwino ndi mphotho, ngakhale pambuyo pa imfa yake.

Chinthu Chabwino Kwambiri Chomwe Munthu Angasiye Pambuyo Iye Atamwalira

Rasulullah Swallallahu alaihi wasallam adati: “Zinthu zabwino kwambiri zomwe munthu angasiye pambuyo iye atamwalira zilipop zitatu: mwana owopa Allah yemwe akumamupangira duwa iye atamwalira, Sadaqatul-Jaria (Ntchito zabwino zomwe zimapezetsa sawabu ngakhale ochitayo atamwalira) ndi maphunziro a chisilamu (omwe adawapereka kwa anthu ena) zomwe anthu amakhala akupitiriza kuchita iye atamwalira.”

Mu Hadith ina, Mtumiki (swallallahgu alaihi wasallam) adati: “Palibe bambo amene angamupatse mwana wake mphatso yabwino kuposa mphatso ya makhalidwe abwino.”

Mu Hadith inanso, Rasulullah (Swallallahu alaihi wasallam), zatchulidwanso, Alemekezeni ana anu, ndipo aphunzitseni makharidwe abwino.”

Lamulo la Quran Majiid 

Kuika mfundo za diini mwa ana anu ndi ntchito yofunika kwambiri kwa makolo, kotero kuti Allah olemekezeka ndi wamphamvu zonse wawalamura kuti akwaniritse udindo umenewu mu Quraan Majiid. Allah, Odalitsika ndi wapamwambamwamba, akunena:

 يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُوا قُوا أَنفُسَكُمْ وَأَهْلِيكُمْ نَارًا

E inu amene mwakhulupirira! zipulumutseni inu ndi banja lanu kumoto wa Jahannum…

Kunena kwina, atsogolereni akazi anu ndi ana anu ku din ndi kuwateteza kuti asayende njira yosokera. Choncho, pa tsiku la Qiyaamah adzafunsidwanso munthu pa ntchito ndi udindo umenewu.

Dua ya Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam), ndi Nabiy Dawood alaihis salaam.

Zanenedwa kuti mwa ma dua omwe Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adauphunzitsa Ummah kuti udziteteze kwa ana opanduka ndi iyi:

اللَّهُمَّ إِنِّي أَعُوذُ بِكَ مِنْ جَارِ السُّوْءِ وَمِنْ زَوْجٍ تُشَيِّبُنِي قَبْلَ الْمَشِيْبِ وَمِنْ وَلَدٍ يَكُوْنُ عَلَيَّ رَبَّا

O Allah! Ndikudzitchinjiriza mwa Inu kwa neba oipa, kwa mkazi amene adzapangitse tsitsi langa kukhala imvi ndisanakalambe, ndi kwa mwana amene adzandigonjetse (ndi Kundipweteketsa chifukwa chomumvera).

Momwemonso zanenedwa kuti mwa ma dua omwe Nabiy Dawuud alaihis salaam ankapanga ndi monga:

اللَّهُمَّ إِنِّي أَعُوذُ بِكَ مِنْ جَارِ السُّوْءِ وَمِنْ زَوْجٍ تُشَيِّبُنِي قَبْلَ الْمَشِيْبِ وَمِنْ وَلَدٍ يَكُوْنُ عَلَيَّ وَبَالاً

O, Allah! ndikudzitchinjiriza mwa inu ku chuma chimene chidzakhala mayeso kwa ine ndi kwa mwana amene adzakhala tsoka kwa ine.

Kupyolera muhadith yake ya yolemekezeka ndi makhalidwe ake apamwamba, Mtumiki (Swallallah alaihi wasallam) adawaphunzitsa maSwahaabah Radhwiyallahu anhum ndi Ummah m’mene angawapatsire ana awo makhalidwe abwino ndi miyambo yachipembedzo ndi kukhanzika m’mitima mwawo makhalidwe abwino achisilamu.

Kuphunzitsa Mwana Makhalidwe Abwino M’magawo Osiyanasiyana a Moyo

Pali mbali zambiri za moyo zomwe ziyenera kuyang’anidwa kwambiri pophunzitsa mwana makhalidwe abwino.
Ena mwa magawowa ndi awa:

1. Kumphunzitsa mwanayo zikhulupiriro zolondora za Chisilamu ndi kumulimbikitsa Imaan. 2. Kuika mwa mwana kufunika kokwaniritsa maufulu a Allah Wamphamvu zonse ndi kupewa machimo.

3. Kutsindika pa mwana kufunika kokwaniritsa ma ufulu a zolengedwa.

4. Kuphunzitsa mwana ulemu, miyambo ndi makhalidwe abwino pokhala ndi anthu.

5. Kuunikira kwa mwanayo kufunika kokhala oyera kunja ndi mkati momwe.

6. Kukhanzikitsa hayaa ndi kuopa Allah mwa mwana.

7. Kutsindika pa mwanayo kufunika kocheza ndi anthu abwino nthaŵi zonse ndi kupewa kukhala limodzi ndi anthu ochita zoipa.

8. Kuphunzitsa mwanayo njira zapadera zopezera chifundo cha Allah Wamphamvu zonse.

Check Also

Kufunikira Koti Mwana Adzicheza Ndi Anthu Abwino

Mu kulera mwana, ndi zofunika kwambiri kuti makolo azionetsetsa kuti mwana wawo nthawi zonse apezeka …