Nthawi ina Mughiirah bin Shu’bah (Radhwiyallahu ‘anhu) atakhala pamodzi ndi anthu ena mu Musjid ya ku Kufah, Sa’eed bun Zayd (radhwiyallahu ‘anhu) adalowa mu mzikiti. Mughiirah (Radhiyallahu ‘anhu) adamulonjera ndipo mwaulemu adamupempha kuti akhale pansi pa nsanja yomwe idali patsogolo pake.
Patapita nthawi pang’ono, munthu wina wa ku Kufah adalowa munzikitimo nayamba kunyoza ndi kuyankhula zoipa za munthu wina wake. Sa’eed bun Zaid (Radhwiyallahu ‘anhu) adamufunsa Mughiirah (radhiyallahu ‘anhu) kuti: “Kodi munthu ameneyu akunena ndani?” Mughiirah (radhwiyallahu ‘anhu) anayankha kuti: “Akunyoza Ali bun Abi Taalib (radhwiyallahu ‘anhu).”
Sa’eed bun Zaid (Radhiyallahu ‘anhu) adakwiya kwambiri ndipo adamutcha Hazrat Mughiirah (radhwiyallahu ‘anhu) dzina lake katatu kuti, “Iwe Mughiirah bun Shu’bah! Iwe Mughiirah bun Shu’bah! Iwe Mughiirah bun Shu’bah!” Kenako adati: “N’chifukwa chiyani ndikumva maswahaaba a Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam) akunyozedwa pamaso panu, inu mukungokhala chete osamuletsa munthuyo?” Ndikuchitira umboni kuti ndidamva Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) akutchula Hadith (yokhudza ma Swahaabah ake). Ndidamva Hadith imeneyi ndi makutu anga. Mtima wanga udasunga mawu amenewo, sindidzapachika bodza lieilonse ma swahaabah radhwiyallah anhu lomwe lidzapangitse kuti adzandifunse pa tsiku la Qiyaamah.
Sa’iid bun Zaid (radhwiya Allahu ‘anhu) ananenanso kuti: “Ndidamva Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) akunena kuti, ‘Abu Bakr ndi wa ku Jannah; Umar ndi wa ku Jannah; Ali ndi wa ku Jannah; Uthmaan ndi wa ku Jannah; Talhah ndi wa ku Jannah; Zubair ndi wa ku Jannah; ‘Abbair ndi wa ku Jannah;’ Sa’d al-Maalik; (ie Sa’d bin Abi Waqqaas) ndi wa ku Jannah Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) ndipo adatchura dzina la munthu wachisanu ndi chinayi ndikumuuzanso nkhani yabwino ya ku Jannah, ndipo ngati ndikufuna kutchura dzina lake pompano, nditha kutero.”
Asilamu omwe adasonkhana mu mzikiti wa Kufah panthawiyo adamupempha kuti: “E, iwe sahabi wa Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam), chonde tidziwitse kuti wachisanu ndi chinayi ndindani.
Sa’iid bun Zaid (Radhwiya Allahu ‘anhu) anayankha kuti: “Popeza inu anthu mwandifunsa m’dzina la Allah Ta’ala, ndikudziwitsani. Ine ndine munthu wachisanu ndi chinayi (amene adapatsidwa nkhani yabwino ya Jannah ndi Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam) ndipo wakhumi adali ndi Mtumiki Swallallahu alaihi wasallam. Abu Ubaidah sanapezeke koma adali nawo pa mkumano wina umene Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) adauza nkhani yabwino ya Jannah ma Sahaabah khumi kuphatikizanso iyeyo).”
Nthawi ina Hazrat bin Zaid (Radhwiya Allaahu ‘anhu) akulankhula kwa anthu, adalumbira nati: “Nkhondo imodzi yomwe Sahaabi adatengana ndi Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam), nkhope yake ndi kubisika ndi fumbi, ndiyaikulu komanso yabwino kwambiri (pamaso pa Allah kuposa inu omwe simuli). Sahaabi), ngakhale mutapatsidwa moyo wa Nuh (‘alaihis salaam) [ndipo ndikukhala moyo wanu onse mukuchita zabwino].” (Musnad Ahmad #1629).