Hazrat Umar (radhwiyallahu ‘anhu) – munthu yemwe dzina lake loyera ndi njira yolemekezera chisilamu, ndipo changu cha imaani chinali chotere mpaka lero, patadutsa zaka 1300, anthu osakhulupirira amamuopabe,adali otchuka chifukwa chowazunza Asilamu (iyeyo) asanalowe Chisilamu. Adapitilizanso kufunafuna mipata yomupha Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam).
Tsiku lina maquraish adasonkhana. (adayitanitsa munthu odzipereka) adati: “Kodi alipo pano amene angakwanitse kumupha Muhammad (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam)?” Hazrat Umar (Radhwiyallahu ‘anhu) adadzipereka nati, “Ndigwira ntchito imeneyi.” Zitatero, anthuwo anafuula kuti: “Ndithudi, iwe ndiwe munthu okhoza kuchita zimenezo, iwe Umar!
Lupanga lake litalendewera m’khosi mwake, Hazrat Umar (Radhiyallahu ‘anhu) ananyamuka kukakwaniritsa ntchito yoipayi. Komabe ali m’njira anakumana ndi Hazrat Sa’d bin Abi Waqqaas (radhwiyallahu ‘anhu) ochokera ku banja la Zuhra (malinga ndi olemba nkhani ena adakumana ndi Sahaabi wina osati Sa’d [radhiyallahu ‘anhu]).
Atakumana ndi Umar (Radhwiya Allaahu ‘anhu), Sa’d (Radhwiyallahu ‘anhu) adamufunsa: “Oh Umar, ukupita kuti?” Umar (radhwiya Allahu ‘anhu) adayankha kuti, “Ndikukamupha Muhammad (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) Allah ateteze!).”
Kenako Sa’d (Radhwiyallahu ‘anhu) adati: “Kodi siukuona kuti banja la Banu Haashim, Banu Zuhrah ndi Banu Abdi Manaf adzakupha pobwezera?”
Atamva yankho ili, Umar adakhumudwa ndipo adati: “Zikuoneka kuti iwenso wasiya chipembedzo cha makolo ako (ndikulowa chisilamu)! Ndiyambira iweyo ndikuphe kaye!”
Atayankhula izi, Umar (Radhwiyallahu ‘anhu) anasolora lupanga lake. Sa’d (Radhwiyallahu ‘anhu) adati: “Inde, inenso tsopano ndi Msilamu!” ndipo atayankhula izi anasololanso lupanga lake. Atatsala pang’ono kuyamba kumenyana pamene Sa’d (Radhiyallahu ‘anhu) adati: “Ukonze kaye nyumba yako. Mlongo wako ndi mlamu wako onse alowa Chisilamu.”
Atamva izi Umar (Radhiyallahu ‘anhu) adakwiya kwambiri ndipo nthawi yomweyo adapita kunyumba kwa mlongo wake. Chitseko cha nyumbayo chidatsekedwera mkati, ndipo mwamuna ndi mkazi onse ankaphunzira Qur-aan kuchokera kwa Khabbab (radhwiyallahu ‘anhu).
Hazrat Umar (Radhiyallahu ‘anhu) adagogoda pachitseko ndikufuula kuti mlongo wake atsegule. Atamva mawu a Umar (radhiyallahu bu) Khabbab (radhwiyallahu ‘anhu) anabisala ndikubisanso Qur’aaniyo.
Mlongo wake atatsegula chitseko, Umar (Radhwiya Allahu ‘anhu) adamumenya m’mutu mwake, ndipo adayamba kutuluka magazi, adamuuza kuti: “E, iwe mdani wa iwe mwini, wasiya chipepmbedzo chako! Kenako Umar (Radhwiya Allaahu ‘anhu) adalowa m’nyumba ndikufunsa: “Mukuchita chani, nanga mlendo amene ndinamumva kunja anali ndani?” Mlamu wake anayankha kuti, “Timayankhulana tokhatokha.
Umar (Radhwiya Allaahu ‘anhu) adati kwa iye: “Kodi iwenso wasiya chipembedzo chako ndi kukalowa m’chipembedzo chatsopanochi?” Mlamu wake anayankha nati, “Koma bwanji ngati chipembedzo chatsopanochi chiri chipembedzo choona?” Atamva izi Umar (Radhwiya Allahu ‘anhu) adamukoka mlamu wakeyo ndevu zake ndikumuukira ndikumugwetsa pansi ndikumumenya koopsa.
Mlongo wake ataloŵerera kufuna kupulumutsa mwamuna wake, anam’menya mbama mwamphamvu kwambiri moti nkhope yake inayamba kutuluka magazi. Popeza anali, pambuyo pa zonse, anali Mlongo wake wa Umar (radhiyallahu ‘anhu), anafuula kuti, “Umar! Tikumenyedwa chifukwa cholowa chisilamu, ndithu, ife talowa chisilamu ndipo utha kutipanga chilichonse chomwe ukufuna!
Pambuyo pake maso a Umar (Radhiyallahu ‘anhu) adagwera pa masamba a Qur’aan Majiid omwe adasiyidwa ndi Khabbab (Radhwiyallahu ‘anhu). Pa nthawiyi, mkwiyo wa Umar (radhiyallahu ‘anhu) udali utachepa, ndipo adachita manyazi ndi magazi a mlongo wake.
Ataona mapepala a Qur’aan adati: “Chabwino, ndiwonetseni masamba awa ndi chiyani?” Mlongo wake anayankha kuti, “Ayi, ndiwe odetsedwa, ndipo palibe munthu odetsedwa angakhudze masamba awa. Umar (Radhiya Allaahu ‘anhu) adakakamirabe, koma mlongo wake sadali okonzeka kumulora kuti agwire masambawo pokhapokha atapanga wudhu ndi ghusl/kusamba.
Pambuyo pake, Umar (Radhwiyallahu ‘anhu) adakasamba, kenako adatenga masambawo ndikuyamba kuwerenga. mapepalawo adali ndi ma aya a Surah Taha olembedwapo, ndipo adayamba kuwerenga kuyambira koyambirira kwa surayi. Umar (Radhiya Allaahu ‘anhu) atafika pa ndime yotsatirayi, khalidwe lake lonse lidasintha ndipo adali munthu osiyana kotheratu.
Ndithudi, ine ndine Mulungu. Palibe opembedzedwa mwachoonadi koma Ine. Choncho ndipembedzeni, ndipo pempherani Swalah kuti chikhale chikumbukiro Changa. (Surah Taha v. 14)
Kenako Umar (Radhwiya Allaahu ‘anhu) adati: “Chabwino, ndiperekezeni kwa Muhammad (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam).” Hazrat Khabbab (Radhwiya Allaahu ‘anhu) atamva izi adavumbukuka komwe adabisala kuja nati: “E, iwe Umar! Ndi nkhani yabwino kwa iwe! Usiku watha lomwe lidali Lachinayi usiku, Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) adapemphera kwa Allah kuti: “O Allah! Chilimbitseni chisilamu Qur’aan Majiid kudzera mwa Umar kapena Abu Jahal wina aliyense yemwe mungakonde (popeza awiriwa adali anthu octhuka ndi mphavu zawo komanso nzeru zawo),zikuonetsa kuti Allah wayankha dua ya Rasulullah swallallahu alaihi wasllam mokomera iweyo.
Umar radhwiyallahu anhu kenako adapita kwa Rasulullah (swallallahu alaihi wasallam) ndikulowa chisilamu m’mawa wa lachisanu.
Kulowa chislamu kwa Umar (radhwiyallahu anhu) chidali chipsinjo chachikulu kwa ma kuffaar koma asilamu adali adakali ochepa pa nthawiyo ndipo osati Makkah yokha koma Dziko lonse la Arabia linkachizonda chisilamu, anthu osakhulupilira adaonjezera mphavu zawo kulimbana ndi chisilamu, ankakumana ndi kukambirana za momwe angathanirane nacho chisilamu komanso adagwiritsa ntchito njira zosiyanasiyana kulimbana ndi chisilamu.
Zikuimira pomwepa,Pamodzi ndi Umar (radhwiyallahu anhu) asilamu adayamba kuswalira munzikiti wa Haram (Ka’bah).
Abdullah bin Masuud (radhwiyallahu anhu) akuyankhula kunena kuti: “kulowa chisilamu kwa Umar (radhwiyallahu anhu) kudali kupambana kwakukulu kwa asilamu, kusamuka kwake kupita ku Madinah kudali thandizo la Asilamu ndipo kusankhidwa kwake kukhala Khalifah udali mdalitso waukulu kwa Asilamu” (Fazaail A’maal)
Alislaam Yeretsani mtima wanu potsatira chisilamu