Kudzithandiza Komanso Kupanga Istinja (Kutawasa) – Chiyambi

Kufunika Kodziyereta

Chisilamu ndichipembedzo chomwe chili ndi ukhondo Kwambiri, chisilamu chimalimbikitsa ukhondo komanso kudziyeretsa m’magawo onse amoyo wamunthu, Nabi (sallallahu alaih wasallam) adati:

الطهور شطر الإيمان

“Kudziyeretsa nditheka ya chikhulupiliro”[1]

Kotero, chisilamu chationgolera ife ndikutionetsa mokwanira m’mene tingadziyeretsele nkati (mwathupi) ndikunja komwe.

Monga talamulidwa kukhala aukhondo posamalira thupi lathu ndinkamwa, talamulidwanso kukhala aukhondo muuzimu poteteza mitima yathu komanso maganizo athu kumachimo monga:

Kuchita kaduka, kudzikweza, umbombo ndizina, Allah Ta’ala akunena:

قد افلح من تزكى

“Wapambana munthu yemwe wadziyeretsa”[2]

Wina atati abweretse poyera malamulo osiyanasiyana asharia, mwachitsanzo:

Kupanga wuzu ukafuna kuswali, kutsuka mkamwa pogwiritsa ntchito miswak ukangodzuka kumene, usanaswali, mkamwa mukamatuluka fungo lonunkha, usanagone ndizina zotero, kusamba ukafuna kuvala Ihraam kapena kuswali Eid kapena swalah ya Jumuah, wina adzazindikira kuti chisilamu ndichipembedzo chokhacho chomwe chili patsogolo kulimbikitsa ukhondo ndikudziyeretsa m’magawo onse a umoyo wamunthu.

Nabi (sallallahu alaih wasallam) adati: “Zinthu zinayi ndi sunnah ya Atumiki onse  alaihim salaam, kukhala ndimanyazi  (mbali zonse za umoyo wamunthu)  kugwiritsa ntchito miswak, komanso kupanga nikah (kukwatira).”[3]

Tikadzifufuza zinthu zonsezi zatchulidwa muhadithizi tipeza kuti zikugwirizana ndi ukhondo wankati (muuzimu) ndikunja (kuthupi).

Mbali inayi, kuli chenjezo ndi zilango zoopsya zomwe zanenedwa m’mahadith kwa osalabadira za ukhondo, kudzera mu kusalabadira ndikusadzisamalira, munthu udzakhala odetsedwa zomwe zingapangitse kuti swalah ndi Ibadah ina yonse yomwe kudziyeretsa nkofunikira kuti isalandiridwe. Chimodzimodzinso, kusasamala za ukhondo wamkamwa ndithupi, munthu adzakhala akupeleka vuto kwa anthu ena.


[1] عن أبي مالك الأشعري قال قال رسول الله صلى الله عليه وسلم الطهور شطر الإيمان (صحيح مسلم، الرقم: ٢٢٣)

[2] سورة الأعلى: ١٤

[3] عن أبي أيوب رضي الله عنه قال قال رسول الله صلى الله عليه وسلم أربع من سنن المرسلين الحياء والتعطر والسواك والنكاح (سنن الترمذي، الرقم: ١٠٨٠) قال أبو عيسى: حديث أبي أيوب حديث حسن غريب

Check Also

Ma Sunnah Komanso Miyambo Ya Dua 2

2. Popanga dua, kwezani manja anu mofanana ndi pachifuwa chanu (i.e. molingana ndi chifuwa chanu). …