Mwezi wa Zul Hijjah uli mgulu la miyezi inayi yopatulika ya kalendala ya Chisilamu. Miyezi inayi yopatulika imeneyi ndi Zul Qa’dah, Zul Hijjah, Muharram ndi Rajab. Malipiro a ntchito zabwino zochitidwa m’miyezi imeneyi amachulukitsidwa, ndipo machimo amene achitidwa m’miyezi imeneyi nawonso amatengedwa kuti ndi oipitsitsa kwambiri.
Allah Ta’ala akuti:
إِنَّ عِدَّةَ الشُّهُورِ عِنْدَ اللَّهِ اثْنَا عَشَرَ شَهْرًا فِي كِتٰبِ اللِه يَوْمَ خَلَقَ السَّمٰوٰتِ وَالْأَرْضَ مِنْهَا أَرْبَعَةٌ حُرُمٌ
Chiwerengero cha miyezi Pamaso pa Allah ndi khumi ndi iwiri (m’chaka) yomwe adaiika tsiku lomwe Adalenga mitambo ndi nthaka, mwa iyo inayi ndi yopatulika.
Kulemekezeka kwa masiku khumi oyambilira a mwezi wa Zul Hijjah tingakupeze pozindikira kuti Allah adalumbilira masiku khumi oyambirira a Zul Hijjah mu Quraan Majiid, ndipo ubwino wapadera walembedwa mmahaadith a Rasulullah swallallahu alaihi wasallam ofotokoza za masiku amenewa.
Allah akuti:
وَالْفَجْرِ وَلَيَالٍ عَشْرٍ
(Ndikulumbirira) m’bandakucha ndi m’masiku khumi (a Zul Hijjah)
Alislaam Yeretsani mtima wanu potsatira chisilamu