Sunnats Ndi Aadaab Za Mwezi Wa Zul Hijjah

1. Mulimbikire kuchita ibaadah m’masiku khumi oyambirira a Zul Hijjah. Malipiro aakulu atchulidwa pa ibaadah yomwe ingachitike m’masiku khumi amenewa.

Olemekezeka Abdullah bin Abbaas radhwiyallahu anhu wanena kuti Nabiy swallallahu alaihi wasallam adati: “Palibe cholungama chomwe chingachitike tsiku lililonse la chaka chomwe chili chabwino kwambiri kuposa masiku khumi a mwezi wa ZulHijjah.” Ma Swahaabah radhwiyallahu anhum adafunsa: “Ngakhale jihaad?” Rasulullah swallallahu alaihi wasallam anayankha kuti “Ngakhale jihaad, kupatula amene waika moyo wake ndi chuma chake pachiswe (pa jihaad) ndipo osabwerera ndi chilichonse ( kupatula jihaad yomwe imachitika m’masiku khumi a Zul Hijjah ndi yabwino kwambiri kuposa jihaad mkati mwa chaka chonse, kupatula jihaad ya mujaahid amene waphedwa). “

2. Yesetsani kusala kudya mkatikati mwa masiku khumi oyambirira. Kusala kudya tsiku lililonse mwa masiku khumi oyambirira a Zul Hijjah (kupatula la khumi), mudzalandira mphotho ya kusala kudya chaka chonse.

3. Yesetsani kupanga ibaadah yochuluka momwe mungathere mkatikati mwa masiku khumi oyambirira a mwezi wa Zul Hijjah. Kupanga ibaadah mkatikati mwa masiku amenewa umapeza mphotho yopanga ibaadah usiku wa Lailatul Qadr.
Olemekezeka Abu Hurairah radhwiyallahu anahu adanena kuti Rasulullah swallallahu alaihi waslaam adati, “Palibe masiku m’chaka omwe kulambira Allah kuli kokondedwa kwa Iye kuposa masiku khumi a mwezi wa Zul Hijjah. Kusala kudya masiku awa (kupatulapo tsiku la khumi) ndi kofanana ndi mphotho ya kusala kudya kwa chaka chonse, ndipo kuima usiku umodzi wa masiku amenewa kumafanana ndi ndikuyimirira usiku wa Laitul Qadti kuchita ibaadah.”

Olemekezeka Hafsah radhwiyallahu anha akunena kuti Rasulullah swallallahu alaihi wasallam adati sankasiya kuchita zinthu zinayi; kusala kudya tsiku la Aashuraa, kusala kudya masiku khumi oyambilira a Zul Hijjah (kupatula pa 10), kusala kudya masiku atatu a mwezi uliwonse; ndi kuswali ma raka awiri a sunnah isanayambe swalah ya Fajr.

4. Nabi (swallallahu alaihi wasallam) adanena kuti Paradaiso imakhala waajib kwa munthu amene amalambira Allah m’ma usiku asanu. (9 Zul Hijjah), usiku wa Nahr (10 Zul Hijjah), usiku wa Tarwiyah (8 Zul Hijjah), usiku wa Arafah usiku wa Eidul Fitr ndi usiku wa 15 Sha’baan.

Olemekezeka Muaaz bun Jabal (radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Rasulullah (swallallahu alaihi wasallam) adati munthu amene angadzutse ma usiku okwana asanu a mchaka pochita ibaadahJannah imakhala yokakamizidwa pa iye (ma usiku asanu amenewa ndi awa) usiku wa Tarwiyah (pa 8 Zul Hijjrah) usiku wa Arafah (9 Zul Hijjah), usiku wa Nahr (10 Zul Hijjah), usiku wa Eidul Fitr ndi usiku wa 15 Sha’baan

5. Ndi mustahab kwa munthu (yemwe sali mu ihraam) kusala kudya tsiku la Arafah lomwe ndi pa 9 Zul Hijjah. Kupatula kupeza sawabu zosala kudya kwa chaka chonse adzakhululukidwaso machimo a zaka ziwiri.

Olemekezeka Abu Qataadah (radhwiyallahu anhu) adati: Swahaabi wina adamufunsa Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam), Oh Mtumiki wa Allah (swallallahu alaihi wasallam) Kodi malipiro a munthu amene wasala kudya pa tsiku la Aashuraa ndi chiyani?” Adayankha: “Ili ndi malipiro a kusala kudya kwa chaka chonse.” Swahaabah adafusanso, ndi malipiro anji omwe angapeze munthu yemwe wasala kudya pa tsiku la Arafah? Rasulullah (swallallah alaihi wasallam) adayankha nati imafufuta sambi za chaka chimenecho komanso chaka chomwe chadutsa.

Ibnu Umar (radhwiyallahu anhuma) akusimba kuti: “Ndidapita ku Haji pamodzi ndi Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) ndipo Rasulullah (swallallahu alaihi wasallam) sadasale nawo tsiku la Arafah (mkatikati mwa Hajj). Chimodzimodzinso ndidachita Haji pamodzi ndi Umar radhwiyallahu anhu ndipo nayenso Sadasale kudya tsiku la Arafah (mkatikati mwa Haji), ndipo ndidachitaso Hajj ndi Uthman ndipo sadasale kudya tsiku la Arafah (mkatikati mwa Hajj).

6. Tsiku la Arafa chulukitsani kuwerenga dua iyi:

لَا إلٰهَ إلَّا اللهُ وَحْدَهُ لَا شَرِيْكَ لَهُ، لَهُ الْمُلْكُ وَلَهُ الحَمْدُ بِيَدِهِ الخَيْرُ وَهُوَ عَلٰى كُلِّ شَيْءٍ قَدِيْرٌ

Palibe Mulungu wina kupatula Allah Yekha, yemwe alibe mthandizi. Ufumu (wa zolengedwa zonse), ndi wake ndipo kutamandidwa konse ndi kwa Iye. M’manja Mwake (ulamuliro) Mokha muli zabwino zonse ndipo Iye Yekha ali ndi mphamvu Pachilichonse.

7. Tsiku la Arafa munthu aliyense akuyenera kuchita dua. Ili ndi tsiku la lopatulika, lodalitsika kwambiri kuposa masiku khumi a Zul Hijah. Zanenedwa kuti Olemekezeka Ali radhwiyallahu anhu adanena kuti pa tsikuli Allah amamasula anthu ambiri kumoto wa Jahannum kuposa tsiku lina lililonse. Ali yemweyo radhwiyallahu anhu ankachita dua iyi tsiku la Arafah ndipo adawalimbikitsa ena mwa maswahaaba kuti azichita duayi:

اللهُمَّ أَعْتِقْ رَقَبَتِي مِنَ النَّار وَأَوْسِعْ لِيْ مِنَ الرِّزْقِ الحلَالِ وَاًصٌرِفْ عَلٰى فِسْقَةِ الْجِنِّ وَالْاِنْسِ

O Allah! Ndichotsereni goli pakhosi langa kumoto wa Jahannam, Ndidalitseni ndi riziki Lochuluka, ndipo Ndichotsereni ziwanda ndi anthu oipa ndi otuluka M’chilamulo chanu.

8. Haaji (Munthu yemwe akuchita Hajj) adzawerenga mawu awa kokwana ka 100 pamene ku Arafa pa 9.

لا إِلَهَ إِلَّا اللَّهُ وَحْدَهُ لَا شَرِيكَ لَهُ، لَهُ الْمُلْكُ وَلَهُ الْحَمْدُ وَهُوَ عَلَى كُلِّ شَيْءٍ قَدِيْرٌ

Palibe wopembedzedwa mwachoonadi koma Allah Yekha, yemwe alibe mnzake. Ufumu (wa zolengedwa zonse), ndi wake ndipo kutamandidwa konse ndi kwa Iye. Ndipo iye ndi wakutha pa china cholichonse.

Pambuyo pake adzawerenge Surah Ikhlaas (Qul Huwallah) ka 100, kenako duruud iyi 10:

اللهمَّ صَلِّ عَلَى مُحَمَّدٍ كَمَا صَلَّيْتَ عَلَى إِبْرَاهِيمَ وَعَلٰى آلِ إِبْرَاهِيمَ إِنَّكَ حَمِيدً مَّجِيْدٌ وَعَلَيْنَا مَعَهُمْ

O Allah! Kutani chifundo Chanu chapadera pa Muhammad (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) monga mukutira chifundo pa Ibrahim (alaihis salaam) ndi banja la Ibrahim, Ndithudi Inu ndinu Oyamikirika Kwambiri, Olemekezeka Kwambiri, ndipo (tipatseni chifundo chanu chapadera) pamodzi nawo.

Olemekezeka Jaabir (radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Rasulullah (swallallahu alaihi wasallam) adanena kuti Msilamu aliyense akaima masana pa Arafah kupanga wuquuf, atayang’ana ku qiblah, ndi kuwerenga ma azkaar omwe atchulidwa pamwambawa, Allah amati:

“E inu angelo anga! Mphoto yanji ya kapolo wanga yemwe wawerenga izi? Wandilemekeza, wachitira umboni wanga, wanditchula ukulu wanga, wandilemekeza, wandizindikira, wanditamanda ndipo watumizira duruud kwa Nabi wanga swallallahu alaihiwasallam. Chitirani umboni, inu angelo anga, kuti ndamukhululukira ndipo ndamupatsa mwayi owombora anthu ena, ndipo ngati angapemphe chiombolo cha anthu onsewa omwe ali pano, ndingalandire pempho lakelo.

 

9. Ndi mustahab kwa iwo amene akufuna kupanga qurbaani kuti asawenge zikhadabo zawo kapena kumeta tsitsi lawo kuyambira kumayambiriro kwa mwezi wa Zul Hijjah mpaka nyama yawo ya qurbaani itazingidwa.

Ummu Salamah radhwiyallahu anha adati, Nabi swallallahu alaihi wasallam adati: munthu amene watsimikiza zopha chinyama kupanga qurabni asamete tsitsi lake ndi kuchotsa zikhadabo kuyambira pomwe mwezi wa Zulhijja waoneka mpaka atamaliza qurbaani yake. “

10. Takbeer-e-Tashreeq iwerengedwe ndi amuna ndi akazi kuyambira pa Fajr pa 9 Zul Hijjah mpaka Asr pa 13 Dzul Hijjah. Amuna adzaiwerenga momveka mawu pomwe akazi adzaiwerenga mosatulutsa mawu pakutha kwa Swalaah iliyonse ya fardh (chipindi).

Takbeer-e-Tashreeq ili motere:

اللهُ أَكْبَرُ اللهُ أَكْبَرُ اللهُ أَكْبَرُ لَا إِلَهَ إِلَّا اللهُ اللَّهُ أَكْبَرُ اللَّهُ أَكْبَرُ وَلِلهِ الْحَمْدُ

Allah ndiye wamkulu Palibe opembedzedwa mwachoonadi kupatura Allah, Allah ndiye wamkulu! Allah ndiye wamkulu, ndipo kutamandidwa konse ndi kwa lye.

Zafotokozedwa kuchokera kwa Ali radhwiyallahu anhu kuti ankawerenga Takbeer-e-Tashreeq kuyambira pa Swalah ya Fajri tsiku la Arafah (9th Zul Hijjah) mpaka swalah ya Asr pa tsiku lomaliza la Tashrieq (13 Zul Hijjah).

11. Chulukitsani kuwerenga ma azkaar m’masiku amenewa:

سُبْحَانَ اللَّهِ الْحَمْدُ لِلَّهِ لَا إِلَهَ إِلَّا اللَّهُ اللَّهُ أَكْبَرُ

Ibnu Abbaas radhwiyallahu anhuma akufotokoza kuti Mtumiki adati: “Palibe masiku m’chaka omwe kumupembedza Allah ndikopambanitsitsa kwambiri (m’malipiro) komaso okondedwa kwambiri pamaso pa Allah kuposa masiku khumi oyambilira a mwezi wa Zul Hijjah. Choncho chulukitsani kuwerenga ma tasbeeh, tahmeed,tahleel ndi takbeer. i.e.

سُبْحَانَ اللَّهِ الْحَمْدُ لِلَّهِ لَا إِلَهَ إِلَّا اللَّهُ اللَّهُ أَكْبَرُ.

12. Yemwe qurbaani ndi yokakamizidwa pa iye ayenera kukwaniritsa.

Bibi Aaishah radhwiyallahu anha akusimba kuti Mtumiki swallallahu alaihi wasallam adati: “Palibe chinthu chokondeka kwa Allah kuposa kukhetsa mwazi (kuzinga chinyama) m’masiku a qurbaani. nyama yomwe yaperekedwa nsembe idzabwera pa tsiku lachiweluzo ndi nyanga zake, ubweya wake ndi ziboda zake (kuti ziikidwe pa sikelo). Nsembeyo imalandiridwa kwa Allah magazi ake asanagwere pansi. Choncho kwaniritsani qurbaani ndi ntima onse kuti mukukwaniritsa lamulo la Allah.

Check Also

Ma Sunnah Komanso Miyambo Ya Jumu’ah 4

11. Werengani durood mochuluka. Olemekezeka Aws bin Aws radhwiyallahu anhu akufotokoza kuti Mtumiki (swallallahu alaihi …