Hadith yoyamba
عن أبي هريرة رضي الله عنه قال قال رسول الله صلى الله عليه وسلم أكثر عذاب القبر من البول البول (المستدرك على الصحيحين للحاكم، الرقم: 653)[1]
Sayyiduna Abu Hurairah (radhwiyallahu anhu) akusimba kuti, Nabi (sallallahu alaih wasallam) adati:”Chilango chachikulu (chomwe anthu ambiri amakumana nacho) m’manda ndi chifukwa cha nkodzo (kusasamala nkodzo omwe umadonthekera pathupi komanso unve wina. kotero, wudhu wawo, swalah ndi ibadah ina siidzalandiridwa chifukwa chosowekera ukhondo)”
Hadith yachiwiri:
عن أنس رضي الله عنه قال قال رسول الله صلى الله عليه وسلم تنزهوا من البول فإن عامة عذاب القبر من البول (الترغيب والترهيب، الرقم: 258)[2]
Sayyiduna Anas (radhwiyallahu anhu) akunena kuti: Nabi (sallallahu alaih wasallam) adati:”Talikilanani ndi nkodzo (I.e.usakudonthokereni pathupi kapena chovala), chifukwa choti, chilango chachikulu (chomwe anthu amakumana nacho) m’manda ndichifukwa cha nkodzo (i.e.kusasamala pankhani yokudonthekera nkodzo ndi unve wina)”
Hadith yachitatu:
عن أبي أمامة رضي الله عنه عن النبي صلى الله عليه وسلم قال إتقوا البول فإنه أول ما يحاسب به العبد في القبر (الترغيب والترهيب، الرقم: 265)[3]
Sayyiduna Abu Umaamah (radhwiyallahu anha) akusimba kuti Nabi (sallallahu alaih wasallam) adati:“Apeweni madontho ankodzo (usakudonthekereni mukamadzithandiza), ndithudi, ichi chidzakhala chinthu choyambilira munthu kuwerengetsedwa m’manda.”
Hadith yachinayi:
عن ابن عباس رضي الله عنهما قال: مر النبي صلى الله عليه وسلم بقبرين فقال: إنهما ليعذبان وما يعذبان في كبير أما أحدهما فكان لا يستتر من البول وأما الآخر فكان يمشي بالنميمة (صحيح البخاري، الرقم: 218)
Sayyiduna Ibnu Abbaas (radhwiyallahu anhuma) akusimba kuti Nabi (sallallahu alaih wasallam) anadutsa pamanda awiri, kenako (pokamba zamanda awiriwa) adati: “Anthu awiri amene ali m’mandamu akulangidwa, ndipo sakulangidwa pazifukwa zikuluzikulu ayi, (sikunali kovuta kuti adziteteze). M’modzi mwa iwo sankaziteteza kumadontho ankodzo, ndipo winayo anali wamiseche (ankabweretsa mavuto ndikuchita chinyengo pakati pa anthu).”
[1] هذا حديث صحيح على شرط الشيخين ولا أعرف له علة ولم يخرجاه وله شاهد من حديث أبي يحيى القتات
قال الذهبي في التلخيص: على شرطهما ولا أعلم له علة وله شاهد
[2] قال المنذري: رواه الدارقطني وقال المحفوظ مرسل
[3] قال المنذري: رواه الطبراني في الكبير أيضا بإسناد لا بأس به