
Mfumu yaku Abysinia (Najaashi (rahimahullah)) nthawi ina inatumiza mikondo itatu kwa Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam) ngati mphatso. Atalandira mikondo itatu ija, Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam) adapereka mkondo umodzi kwa Ali (radhwiyallahu ‘anhu), adapereka mkondo wachiwiri kwa Umar (Radhwiyallahu ‘anhu) ndipo adadzisungira yekha mkondo wachitatu (kukhala wake).
Nthawi ya Eid ziwirizi, Bilaal (Radhwiyallahu ‘anhu) ankanyamula mkondo wa Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam) ndikumayenda kutsogolo kwake. Ankayenda kutsogolo kwa Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam) uku atagwira mkondowo posonyeza ulemu kwa Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam).
Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam) ndi Bilaal (radhwiya Allahu ‘anhu) akafika pa bwalo loswalira Eid, Bilaal (radhwiya Allahu ‘anhu) ankazika mkondowo pansi kuti ukhale ngati sutrah kwa Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam) poswali swalah ya Eid.
Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam) atachoka pa dziko lino lapansi ndipo Abu Bakr (Radhwiyallahu ‘anhu) atasankhidwa kukhala khalifah, Bilaal (radhwiya Allahu ‘anhu) amachitanso chimodzimodzi kwa Abu Bakr (radhiyallahu ‘anhu) masiku a Eid. (Siyar A’laam Nubalaa’ 3/221).
Alislaam Yeretsani mtima wanu potsatira chisilamu