Jumuah

Tsiku la Jumu’ah ndi lofunikira kwambiri mu Chisilamu. Izi ndi zina mwa zabwino zazikulu za Allah pa Ummah uwu ndipo ndichinthu chodziwika bwino m’Chisilamu.

Rasulullah (sallallahu ‘alaihi wasallam) adati:

“Tsiku la Jumu’ah ndi sayyidul ayyaam (lomwe ndi mtsogoleri wa masiku onse), ndi tsiku lalikulu kwambiri (kuchokera m’masiku a msabata) pamaso pa Allah Taala. Ndi tsiku lkmwe lili ndi malipiro ochuluka kuposa tsiku la Eidul Adha ndi tsiku la Eidul-Fitr pa maso pa Allah Taala.

“Pali zochitika zisanu zapadera zomwe zikupezeka pa tsiku la Jumu’ah (Choyamba) pa tsikuli Allah Taala adalenga Nabi Aadam (alayhis salaam) Chachiwiri, Allah Ta’ala adamutumiza Adam alaihis salaam pamodzi ndi nkazi wake Hawa dziko lapansi (chachitatu) pa tsiku limeneli Nabii Aadam (alayhis salaam) adamwalira ndipo adabwelera kunyumba yake nyumba yoyambilira). (Chachinayi) pa tsiku la Jumuah pamakhala nthawi yapaderadera (yovomerezeka) yomwe dua iliyonse yomwe kapolo wachita kwa Allah dua yake idzayankhidwa, bola ngati sakupempha chilichonse cha Haramu. (Chachisanu) pa tsiku limeneli, Qiyaamah idzachitika.

“Palibe mngelo amene ali pafupi ndi Allah Taala ngakhale thambo kapena nthaka, phiri lililonse ngakhale nyanja, koma limaopa tsiku la Jumu’ah (chifukwa chakuti Qiyaamah idzachitika tsiku limeneli).

Rasulullah (sallallahu ‘alaihi wasallam) adanena kuti tsiku la Jumuah ndi tsiku lounikira, ndipo usiku wa Jumuah ndi usiku ounikira.

M’ Hadith yake yodalitsika, Rasulullah (sallallahu ‘alaihi wasallam) waulimbikitsa Ummah kuti uzionjezera kuwerenga duruud pa tsiku la Jumu’ah, chifukwa ichi chidzakhala njira yowakhululukira ndi njira yopezera maduwa ake.

Umar bin Khattaab (radhiyallahu ‘anhu) akusimba kuti Mtumiki (sallallahu ‘alaihi wasallam) adati: Ndichulukitsireni kundiwerengera kwa duruud mu usiku ndi usana wa Jumuah chifukwa duruud yanu imaonetsedwa kwa ine. Kenako ndimapempha kwa Allah Taala kuti akukhululukireni machimo anu.”

Check Also

Ma Sunnah Komanso Miyambo Ya Jumu’ah 1

1. Werengani Surah Dukhaan Lachinayi usiku. Olemekezeka Abu Hurairah (radhwiyallah anhu) akunena kuti Rasulullah (swallallahu …