Abstract apocalyptic background - burning and exploding planet Earth in red sky, hell, end of world. Elements of this image furnished by NASA

Momwe Mungadzipulumutsire ku Fitnah (Mayesero)za Dajjaal

M’mahadith odalitsika, Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam) adaupatsa ummah mankhwala odzitetezera ku ma Fitna a nthawi zonse komanso Mayesero a Dajjaal. Zanenedwa kuti Olemekezeka Uqbah bin Aamir (radhwiyallahu ‘anhu) nthawi ina adamufunsa Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam), “Oh Rasul wa Allah (swallallahu ‘alaihi wasallam)! Kodi njira yopezera chipulumutso ndi iti (kuchokera ku ma fitnah onse)?” Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam) anayankha kuti, “Dzitetezeni pa lilime lanu, nyumba yanu iyenera kukhala yokwanira kwa inu, ndipo lirani (ndi kusonyeza chisoni) pa zolakwa zanu ndi machimo anu.” (Sunan Tirmizi #2406)

Mu Hadith iyi, tikupeza kuti Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam) adafotokoza malangizo atatu omwe munthu angapeze chipulumutso kuchokera ku ma fitnah a nthawi zonse komanso ma fitnah a Dajjaal.

1. Khalani M’nyumba Mwanu

Chitsogozo choyamba ndi chakuti munthu ayenera kukhala pakhomo pake ndikupewa kupita malo omwe ma fitnah amapezeka. Rasulullah (sallallahu ‘alaihi wasallam) anafotokoza kuti ma fitnah adzachuluka kwambiri Qiyaamah ikamadzayandikira kotero kuti ngati munthu aliyense kudzera mu kungoona kokha adzamukopa nthawi yomweyo ndikumukokera komweko. Rasulullah (sallallahu ‘alaihi wasallam) anati:

من تشرف لها تستشرفه

Munthu amene angadzatambasule khosi lake kuti aone (chifukwa cha chidwi), idzamukoka. (Saheeh Bukhaari #3601)

Ndi chifukwa chake munthu akuyenra adzipulumutse yekha ndi banja lake, ayenera kuonetsetsa kuti iye ndi banja lake akukhala kutali ndi malo osonkhanira kapena malo omwe ma fitnah ndi uchimo zimapezeka. Mu Hadith ina, Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam) adaulangiza motsindika Ummah kuti udzikhala pakhomo m’mawu awa:

كونوا أحلاس بيوتكم

Khanzikikani mnyumba zanu . (Sunan Abu Dawood #4262)

Mu kuyankhula kwina, monga momwe gawo la pansi pa kapeti limakhanzikikira pansi ndipo silisuntha, momwemonso munthu ayenera kukhala otetezedwa m’nyumba mwake.

2.Samalitsitsani Kwambiri Pa zolankhula Zanu

Chinthu chachiwiri ndichakuti munthu ayenera kusamala kwambiri pa kalankhulidwe, chifukwa kuyankhula ndicho chifukwa choyambitsa fitnah.

Mu Hadith ya Olemekezeka Uqbah bin Aamir (radhwiyallahu ‘anhu) yomwe yanenedwa pamwambapa, ngakhale kuti mawu oti ‘lilime’ agwiritsidwa ntchito, cholinga cha Hadith chimaphatikizaponso kusamala munjira zonse zoyankhulira, chifukwa mawu ndi zolankhula za munthu zimafotokozedwa kudzera munjira izi zoyankhulirana. Popeza kaya ndi foni yam’manja, malo ochezera a pa Intaneti kapena njira ina iliyonse yolankhulirana, munthu ayenera kusamala kwambiri akamagwiritsa ntchito zinthu zimenezi.

Tiyenera kukumbukira kuti pamene Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam) anatiuza kuti tikhale m’nyumba zathu, ndiye kuti popeza munthu akakhala m’nyumba mwake, ndiye kuti sadziwa zambiri za mdziko zomwe zikuchitika kunja, motero amachepetsa mwayi oti agwere mu fitnah zakunja.

Choncho, ngati munthu ali m’nyumba mwake, koma akukumana ndi zochitika zonse zomwe zikuchitika kunja kudzera pa intaneti, foni ndi zina zotero, ndiye kuti ngakhale ali m’nyumba, sasiyana ndi munthu amene sali m’nyumba, chifukwa akukhudzidwa ndi zonse zomwe zikuchitika kunja kwa nyumba ndipo motero amatha kukodwa mosavuta ndi ma fitnah.

3. Khalani Ndi Nkhawa Pa Zofooka Zanu ndi Machimo Anu

Chinthu chachitatu ndichakuti munthu ayenera kukhala odera nkhawa pa zofooka zake ndi machimo ake nthawi zonse ndikuyesetsa mwakhama kuti adzisinthe. Ngati munthu adziganizira mozama, amayamba kuzindikira zofooka zambiri ndi zofooka zomwe ali nazo m’moyo wake. Pambuyo pake, ayenera kulira ndi kulapa machimo ake onse ndikuyesetsa kudzisintha. Munthu akamayang’ana kwambiri zofooka zake ndi machimo ake, sadzayamba kuyesa kupeza zofooka za ena.

4. Igwiritsitseni mwamphamvu Qur’aan ndi Sunnah

Kupatula malangizo atatu omwe atchuridwa pamwambapa, mma Ahaadith ena, Rasulullah (sallallahu ‘alaihi wasallam) adaulamula ummah kuti ugwiritsitse mwamphamvu Qur’aan Majeed ndi Sunnah ngakhale zitakhala kuti akumana ndi mavuto owopsya omwe angakumane nawo. Rasulullah (sallallahu ‘alaihi wasallam) adati:

Ndithudi, mudzakhalabe pa chiongoko chamngwiro kuchokera kwa Mbuye wanu, bola ngati kuledzera kwa zinthu ziwiri sikukugonjetsani; kuledzera kwa umbuli, ndi kuledzera kwa chikondi cha zinthu zapamwamba (za dziko lapansi). Pakadali pano mukulamula anthu kuchita zinthu zabwino, kuwaletsa kuchita zoipa ndi kuyesetsa (ndi kuchita jihaad) chifukwa cha Dini. Chikondi cha dziko lapansi chikakugonjetsani, ndiye kuti simudzalamulanso anthu kuchita zinthu zabwino, kuwaletsa kuchita zoipa ndi kuyesetsa kuchita zinthu zabwino. Anthu amene akugwiritsitsa mwamphamvu Qur’aan Majiid ndi Sunnah panthawiyo adzakhala ngati Muhaajiriin ndi Ansaar (radhwiyallahu ‘anhum) kumayambiriro kwa Chisilamu. (Musnad Al-Bazzaar #2631, Majma’-uz- Zawaaid #12159)

5. Pewani Kutengera Njira za Makafiri

Mu mahaadith zlambiri, Ummah wachenjezedwa ndi kuletsedwa kutengera njira za makafiri ndikuwatsata mmaonekedwe awo ndi chikhalidwe chawo. Kupyolera mu kutsanzira za makafiri, munthu adzagwera muzolakwa zawo ndi zolakwa zawo.

Olemekezeka Umar (radhwiyallahu ‘anhu) adanenapo kale kuti, “Pewani kutengera adani a Allah Ta‘ala, Ayuda ndi Akristu, m’zikondwerero zawo, chifukwa mkwiyo wa Allah Ta‘ala umawagwera. Ndikuopa kuti (ngati muwatsanzira m’njira zawo kapena kutenga nawo mbali m’zikondwerero zawo,) mkwiyo wa Allah Ta‘ala udzakugwerani. Pamene simukudziwa momwe alili mkati mwawo (ndi chidani chomwe ali nacho pa Chisilamu m’mitima mwawo), ndiye bwanji mukutsatira njira zawo ndi machitidwe awo?!” (Shu’abul Imaan #8940)

Chimodzimodzinso, Abdullah bin Amr (radhwiyallahu ‘anhuma) adanenapo kale kuti, “Amene amakhala m’dziko la osakhulupirira, kutenga nawo mbali m’zikondwerero zawo ndi kuwatsanzira mpaka atamwalira ali m’mkhalidwe umenewo, adzaukitsidwa nawo pa Tsiku la Qiyaamah.” (Al-Muhazzab fikhtisaari Sunanil Kabeer #14659)

6. Werengani Surah Yasiin ndi Surah Kahf

Kuti tipeze mtendere wa mumtima ndi m’maganizo komanso chitetezo ndi madalitso a deeni, Rasulullah (sallallahu ‘alaihi wasallam) anatilimbikitsa kuwerenga Surah Yasiin tsiku lirilonse ndi Surah Kahf Lachisanu lirilonse. Ngati munthu aganizira mavesi a Surah ziwirizi, ndiye kuti adzapeza kuti mutu wa Surah Yasiin ndi Moyo osatha, pomwe mutu wa Surah Kahf ndi momwe achinyamata a m’phangamo adadzitulutsira ku ma fitnah ndikukhalabe olimba pa Deen. Chifukwa chake, powerenga Surah izi, munthu ayenera kutero ndi chiyembekezo chakuti Allah Ta‘ala adzatidalitsa ndi zabwino za Moyo osatha ndipo adzatipatsa chitetezo chaumulungu ku fitnah za dziko lino ndi lotsatira.

Check Also

Zizindkiro za Qiyaamah 5

Chikhulupiriro cha Ahlus Sunnah wal Jamaa’ah pa nkhani ya Dajjaal Kutulukira komanso kubwera kwa ma …