
Olemekezeka Abu Zar (radhwiyallahu ‘anhu) atatsala pang’ono kumwalira, panalibe wina aliyense kupatula mkazi wake ndi kapolo wake. Anawalangiza kuti, “Mundisambitse ndi kundiveka sanda (ndikamwalira). Kenako tengani thupi langa ndi kuliyika pamsewu. Uzani gulu la anthu lomwe liyambilire kudutsa kuti, “Uyu ndi Abu Zar (radhwiyallahu ‘anhu),Otsatira wa Rasulullah (swallallahu ‘alayhi wasallam). Tithandizeni kumuika m’manda.”
Atamwalira, onse awiri anachita monga momwe adawalangizira (monga kumusambitsa ndikumuveka sanda ndipo kenako kuika mtembo wake pansewu).
Gulu loyamba la anthu oyenda pansi linali gulu la Abdullah bin Mas’ood (radhwiyallahu ‘anhu). Iye adali paulendo opita ku Makkah Mukarramah kukachita Umrah limodzi ndi anthu ena ochokera ku Iraq.
Akudutsa, anadabwa kuona mtembo utagonekedwa panjira ndipo adachita mantha kuti ngamila zingaonde. Pamenepo, kapolo wa Abu Zar (radhwiyallahu ‘anhu) anabwera nati kwa anthuwo, “Uwu ndi mtembo wa Abu Zar, Otsatira wa Nabi (Swallallahu ‘alayhi wasallam). Tithandizeni kuti timuike m’manda.”
Atamva izi Abdullah Ibn Masood (Radhwiya Allahu ‘anhu) anayamba kulira nati: “Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam) ananena zoona pamene adanena (Pa nkhondo ya Tabook) kuti, “E, Abu Zar! Wayenda wekha (kuti udzakhale nafe pa nkhondo ya Tabook), udzamwalira wekha ndipo udzaukitsidwa wekha.”
Kenako anatsika ngamila zawo ndikupita kukamuika m’manda.
Alislaam Yeretsani mtima wanu potsatira chisilamu