binary comment

Kudya

Chisilamu ndi Dini ya padziko lonse. Ndi ya nthawi zonse, malo onse ndi anthu onse. Ndi yangwiro komanso yokwanira, kotero kuti yamuonetsa munthu njira yokwaniritsira malamulo a Allah ndi ufulu wa akapolo ake.

Munthu asadafike m’dziko kufikira kumwalira, Chisilamu chakhazikitsa malamulo ndi ziletso zomwe zingamuchititse kuti akhale osangalala.

Kupatura kupemphera komwe ndi njira yopezera mtendere opanda malire wa Allah. Chisilamu chamuphunzitsa munthu njira yosinthira ngakhale zochitika zake zapadziko lapansi kukhala ntchito za ibaadah zomwe kudzera mwa izo adzatha kukondweretsa Allah ndikukhala gwero la chifundo kwa anthu.

Pomwe tili padziko lapansi, munthu aliyense ayenera kudya, kumwa, kugona, kuchita malonda, kuyanjana ndi anthu ndikukwaniritsa zosowa zina. Komabe, kudzera mukuchita zinthu izi motsatira njira ya sunnah, munthu adzatha kupeza mphotho zambiri ndi kuteteza mwayi odziyandikitsira kwa Allah ndi Mtumiki Wake okondedwa.

Masunnah Ndi Miyambo Ya Pakudya

Ma Sunnah ndi Miyambo Musanayambe kudya

1. Nthawi zonse idyani chakudya cha halaal komanso chopatsa thanzi. Pewani kudya chakudya chokaikitsa kapena cha haraam.

2. Idyani ndi cholinga chofuna kupeza mphamvu kuti muthe kukwaniritsa malamulo a Allah ndikumupembedza.

3. Munthu ayenera kukhala pansi ndikumadya.

4. Yalani nsalu (dastarkhaan) pansi musanayambe kudya.

Qataadah rahimahu-Allah adafunsidwa kuti: “Kodi iye Mtumiki swallallah alaihi wasallam ndi ma Swahaabah ankakonda kudya motani? Qataadah rahimahu-Allah adayankha: “Iwo ankakonda kudyera pa dastarkhaan (choyala pansi).