Chitsimikizo Cha Sayyiduna Abdullah bin Mas’ood (radhiyallahu ‘anhu) Pa Mawu a Rasulullah (sallallahu ‘alaihi wasallam)

Ulendo wina, nthawi ya khilaafat yake, Sayyiduna Uthmaan (radhwiyallhu ‘anhu) anabwera kudzacheza ndi Olemekezeka Abdullah bin Mas’ood (radhiyallahu ‘anhu). Apa ndikuti Abdullah bin Masood (radhwiyallahu ‘anhu) akudwala matenda ake omaliza. Sayyiduna Uthman (radhwiyallahu ‘anhu) anamufunsa kuti, “Ndi vuto lanji lomwe likukusautsa?”

Abdullah bin Mas’ood (radhiyallahu ‘anhu) anayankha kuti, “Chomwe chikundisautsa padakali pano ndi nkhawa yokhudza kudzayankha mlandu pa machimo anga.”

Sayyiduna Uthmaan (radhwiyallahu ‘anhu) kenako anamufunsa kuti, “Kodi uli ndi khumbo lililonse loti ndikwaniritse?” Iye anati, “Padakali pano, chomwe ndikufuna ndi chifundo cha Mbuye wanga.”

Pambuyo pake Uthmaan (radhwiyallahu ‘anhu) adamufunsa kuti, “Kodi ndipeze dokotala kuti akuthandize?” Iye anayankha kuti, “Dokotala weniweni ( Allah Ta’ala amene ali ndi mphamvu zochiritsa) ndi amene wandipangitsa kudwala.”

Kenako Uthmaan (radhwiyallahu ‘anhu) adamufunsa kuti, “Kodi ndikupatseko ndalama kuchokera ku chuma cha boma zoti uthandizikire?” Iye anayankha kuti, “Pakadali pano sindikusowekera çhilichonse.”

Uthmaan (radhwiyallahu ‘anhu) adati, “Mwina zithandiza ana ako aakazi.” Abdullah bin Masood (radhwiyallahu ‘anhu) anati, “Kodi mukuopa kuti umphawi ungawasowetsw ntendere ana anga aakazi? Ndawalangiza kuti aziwerenga Surah Waaqiah usiku ulionse, malinga ndi mmene ndinamumvera Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam) akunena kuti, ‘Amene amawerenga Surah Waaqiah usiku ulionse, umphawi siudzamukhuza konse.” (Usdul Ghaabah 3/381)

Check Also

Abdullah bin Mas’uud (radhwiyallahu ‘anhu)

Olemekezeka Abdullah bin Mas’uud (radhwiyallahu ‘anhu) anali mnyamata wamng’ono, akuweta mbuzi za Uqbah bin Abi …