Ma Dua Onena Ukamaliza Kudya 2

Dua 6

اَلْحَمْدُ للهِ الَّذي أَطْعَمَ وَلَا يُطْعَمُ مَنَّ عَلَيْنَا فَهَدَانَا وَأَطْعَمَنَا وَسَقَانَا وَكُلُّ بَلاَءٍ حَسَنٍ الحَمْدُ لِلهِ الَّذِي أَطْعَمَ مِنَ الطَّعَامِ وَسَقَى مِنَ الشُّرْبِ وَكَسَا مِنَ الْعُرۡيِ وَهَدٰى مِنَ الضًّلاَلَةِ وَبَصَّرَ مِنَ العَمٰي وَفَصَّلَ عَلٰى كَثِيرٍ مِمَّنْ خَلَقَ تَفْضِيْلاً ألْحَمْدُ للهِ رَبِّ الْعَالَمِين

Kuyamikidwa konse ndi kwa Allah amene amadyetsa ndipo sadyetsedwa. Adatipatsa mtendere Wake ndipo adationgolera kunjira yoongoka, ndipo Adatipatsa chakudya ndi chakumwa, ndipo ubwino ulionse Watichitira. Kuyamikidwa konse ndi kwa Allah yemwe watipatsa chakudya kuti tidye, kutipatsa chakumwa, kutiveka umaliseche, Yemwe adationgola (ife) ndi kutichotsa ku kusokera, watipenyetsa ndi kutichotsa ku khungu, ndipo watidalitsa kwambiri kuposa zolengedwa zake zambiri. Mbuye wa zolengedwa.

Zindikirani: Dua yomwe tatchulayi iyenera kunenedwa mukatha kudya, pamene munthu akusamba m’manja.

Dua 7

اللَّهُمَّ أَطْعَمْتَ وَأَسْقَيْتَ وَأَغْنَيْتَ وَأَقْنَيْتَ وَهَدَيْتَ وَأَحْيَيْتَ فَلَكَ الْحَمْدُ عَلَى مَا أَعْطَيْتَ

Oh Allah Talaa! Mudatipatsa chakudya kuti tidye, ndipo mudatipatsa chakumwa, ndipo mudatipatsa chuma, ndipo mudatipatsa kukhutira, ndipo mudatitsogolera, ndipo mudatidalitsa ndi moyo, kotero kuti ndi kwa Inu nokha kuyamika konse pa zomwe mwatipatsa!

Dua 8

الْحَمْدُ لِلَّهِ الَّذِي هُوَ أَشْبَعَنَا وَأَرْوَانَا وَأَنْعَمَ وَأَفْضَلَ

Kuyamikidwa konse ndi kwa Allah Yemwe watikhutitsa, watithetsera ludzu, Watidalitsa ndi zabwino ndi kutidalitsa ndi chisomo Chake chapadera.

Zindikirani: Powerenga dua yomwe yatchulidwa pamwambayi mutamaliza kudya, kudzalembedwa kuti mwasonyeza kuthokoza ndi kuyamika kwa Allah Talaa chifukwa cha chakudya chimene mwadya.

Check Also

Kudya

Chisilamu ndi Dini ya padziko lonse. Ndi ya nthawi zonse, malo onse ndi anthu onse. …