
Hazrat Abdullah ibn Mas’uud (radhiyallahu anhu) adali munthu oyamba kuwerenga Qur’aan Majeed mokweza mawu ku Makkah Mukarramah Aquraish asanalowe Chisilamu.
Tsiku lina, maSwahaabah (radhiyallahu anhum) anasonkhana nati, “Ndikulumbira mwa Allah, Aquraish sanamvepo wina akuwerenga Qur’aan mokweza mawu pamaso pawo, ndiye ndani pakati pathu amene ali okonzeka kupita kukawerenga Qur’aan mokweza pamaso pawo?”
Hazrat Abdullah bin Mas’uud (radhiyallahu ‘anhu) adati, “Ndipita ndikawerenge Qur’aan mokweza pamaso pawo.” Maswahaabah (radhiyallahu anhum) adayankha kuti, “Tikuopera moyo wako! Tikufuna kuti munthu yemwe apite kwa iwo ndi kuwerenga Qur’aan mokweza akhale yemwe ali ndi fuko lamphamvu lomwe likamuteteza kwa iwo ngati akufuna kumua.” Hazrat Abdullah bin Mas’uud (radhiyallahu ‘anhu) adayankha, nati, “Ndiloreni ndipite Allah akateteza moyo wanga!”
Tsiku lotsatira chaku m’mawa, Hazrat Abdullah (radhiyallahu ‘anhu) ananyamuka nafika pa Maqaam-e-Ebrahi. Panthawiyo, Aquraish anali atasonkhana cha pafupi. Anayima pafupi ndi Maqaam-e-Ebrahimnayamba kuwerenga Qur’aan Majiid mokweza. Anayamba ndikuwerenga Bismillah, kenako anayamba kuwerenga Surah Rahmaan.
Aquraishi anamvetsera kuwerenga kwake mwachidwi, kenako anayamba kufunsana kuti, “Kodi Ibnu Umm-e-Abd (kunena Hazrat Abdullah bin Mas’uud) akuwerenga chani?” Ena mwa iwo anayankha kuti, “Akuwerenga ma vesi ena omwe Muhammed wawabweretsera.” Atamva izi, anaimirira nayamba kumumenya kunkhope. Komabe iye anapitiriza kuwerenga Qur’aan Majeed momwe anakwanitsira kuwerenga pamaso pawo.
Zonse zitatha, Hazrat Abdullah (radhiyallahu ‘anhu) anabwerera kwa anzake nkhope yake itavulazidwa chifukwa cha kumenyedwa. Atamuona anzake anati kwa iye, “Timaopa izi kuti zikuchitikira!” Iye anayankha kuti, “Adani a Allah Ta’ala ndi osafunika kwambiri kwa ine tsopano kuposa kale (izi zachitika ndipo sindikusamala za momwe akundionera – m’malo mwake ndipitilizabe kuwerenga Qur’aan Majiid pamaso pawo). Ngati mukufuna kuti ndipite ndikawerenge Qur’aan kachiwiri pamaso pawo, ndiine okonzeka kupitanso mawa ndikachite zimenezo.” Anzakewo adati kwa iye, “Izi zakwanira! Tinkafuna kuti wina awapangitse kumva kuŵerenga kokongora, ndipo wakwaniritsa izi powapangitsa kumva, koma tsoka ilo iwo safuna kumva.” (Usdul Ghaabah 3/381)
Alislaam Yeretsani mtima wanu potsatira chisilamu