Dua Yoyamba
اَلْحَمْدُ لِله الَّذِي أَطْعَمَنَا وَسَقَانَا وَجَعَلَنَا مُسْلِمِينَ
Kuyamikidwa konse ndi kwa Allah amene watipatsa chakudya ndi chakumwa ndi kutipanga kukhala Asilamu.
Dua Yachiwiri
الْحَمْدُ لِلَّهِ الَّذِي أَطْعَمَنِيْ هَذَا الطَّعَامَ وَرَزَقَنِيْهِ مِنْ غَيْرِ حَوْلٍ مِّنّّي وَلاَ قُوَّةٍ
Kuyamikidwa konse ndi kwa Allah amene wandipatsa chakudya ichi kuti ndidye, ndipo wandipatsa popanda kuvutikira kulikonse kapena kuyesetsa kumbali yanga.
Dziwani izi:
Olemekezeka Mu’aaz bun Anas radiyahallhu akusimba kuti Mtumiki sahallualyahi wasallam adati: “Amene angadye chakudya chilichonse, kenako ndikuwerenga duwa yomwe yatchulidwa pamwambayi, machimo ake a m’mbuyo (ang’onoang’ono) ndi amtsogolo amakhululukidwa.
Duwa Yachitatu
الْحَمْدُ لِلَّهِ الَّذِي أَطْعَمَ وَسَقَى وَسَوَّغَهُ وَجَعَلَ لَهُ مَخْرَجًا
Kuyamikidwa konse ndi kwa Allah Talaa yemwe watipatsa chakudya ndi kutipatsa chakumwa, nachititsa (chakudya ndi zakumwa) kupita kum’mero mosavuta, ndi kupanga malo otuluka (kuti zonyasa zichoke matupi athu).
Dua Yachinayi
اللَّهُمَّ بَارِكْ لَنَا فِيْهِ وَأَطْعِمْنَا خَيْرًا مِّنْهُ
O Allah Talaa ikani baraka mu chakudyachi ndipo tipatseni zabwino kuposa izi.
Dua Yachisanu
الْحَمْدُ لِلَّهِ الَّذِي كَفَانَا وَأَرْوَانَا غَيْرَ مَكْفِي وَلَا مَكْفُوْرٍ
Kuyamikidwa konse ndi kwa Allah Talaa yemwe watikwaniritsira zosowa zathu ndi kutichotsera ludzu, (O) Allah تَبَارَكَ وَتَعَالَى Sitikuchimva kuti kuyamika kwathu kukukwanira (pokutamandani pa Chakudya chomwe mwatipatsa), ndiponso sitikuonetsa kusakuthokozani (pa zabwino zanu pa ife).
Zindikirani: Rasulullah sawallhu alayhi wa sallam ankawerenga dua yomwe yatchulidwa pamwambayi akamaliza kudya kapena mbale zomwe amadyera zikamachotsedwa.
Alislaam Yeretsani mtima wanu potsatira chisilamu