Kumwa

Pali ma sunnah ndi ma adaab ambiri okhudzana ndi kumwa. Ma sunnah ndi ma adaab ena amakhudzana ndi madua osiyanasiyana omwe alamulidwa kuti awerengedwe usanayambe kumwa, pamene ukumwa komanso utamaliza. Ma sunnah ndi ma adaab ena amakhudzana ndi momwe munthu angamwere.

Kupatula izi, pali ma sunnah ndi ma adaab omwe amamuphunzitsa munthu kuchuluka kwa madzi omwe ayenera kumwa nthawi imodzi kuti asaononge thanzi lake. Popeza kumwa moyenera ndikofunikira, chifukwa izi zingathandize munthu kukhala ndi thanzi labwino lomwe lidzamuthandize kulambira Allah

Munthu akazilingalira ziphunzitso zosiyanasiyana za dini zokhudzana ndi kumwa, adzazindikira kuti gawo ili lokha ndilokwanira kuwulula kukongola ndi ungwiro wa Chisilamu.

Chisilamu chamuonetsa munthu njira yokwaniritsira zosowa zake kuyambira kumwa m’njira yabwino kwambiri ndipo chamuphunzitsa momwe angayamikire Allah chifukwa cha zabwino ndi maubwino Ake osawerengeka.

Kudzera mu kukwaniritsa bwino sunnah yonse ya Rasulullah sawallhu alayhi wasallam m’moyo wa munthu (monga sunnats za pakudya, kumwa, kuvala, kuyanjana ndi anthu, ndi zina zotero), munthu adzadalitsidwa ndi moyo oyera ndipo adzapatsidwa ulemu.

Check Also

Masunnah Ndi Miyambo Ya Pakudya 2

Ma Sunnah ndi Miyambo Musanadye 5. Sambani m’manja musanayambe kudya. Olemekezeka Abdullah bin Abbaas (radhwiyallahu …