Kuyamika Pa Mdalitso Okhala Ndi Moyo

Dawuud bin Dinaar anali Imaam wamkulu pankhani ya Hadith komanso mphunzitsi wa ma Muhadditheen otchuka, monga Imaam shu’bah (rahimahullah) ndi Imaam Wakii (rahimahullah).

Mkatikati mwa moyo wake kunadzabuka mliri ku Khuraasaan kumene ankakhala omwe udakhudza anthu ndipo ambiri adataya miyoyo yawo.

Dawuud bin Dinaar (rahimahullah) anali m’gulu la omwe adagwidwa ndi mliriwu ndipo adadwala. Komabe, popeza Allah sanalembe kuti afe panthawiyo, Allah adamudalitsa ndi shifaa kuchokera ku mliriwu ndipo adapanga matendawa kukhala njira yopitira patsogolo muuzimu.

Akunena kuti mkat8kati mwa matenda ake, nthawi ina adagwa osazindikira, ndipo ali chonwecho adawonetsedwa masomphenya momwe denga la nyumba yake linagawanika ndipo angelo awiri adatsika pa iye kuchokera kumwamba.

Mngelo mmodzi anakhala pambali pake, pomwe wina anakhala kumapazi ake. Mngelo amene anakhala pafupi ndi mapazi ake anayamba kuyang’ana mapazi ake, pomwe mngelo amene anakhala pambali pake anatsegula pakamwa pake ndikuyang’ana lilime lake komanso mkamwa mwake.

Mngelo amene ankayang’ana mapazi ake anauza mngelo amene anakhala kumutu kwake. “Ndapeza kuti nthawi zambiri amagwiritsa ntchito mapazi amenewa poyenda kupita ku mzikiti kukapemphera.”

M’mawu ena, mngeloyo ankatanthauza kuti ali m’gulu la anthu amene amapita ku musjid kukapemphera ndikupeza mphotho yaikulu yomwe yatchulidwa mmahaadith kwa anthu amene amapita ku musjid kuti pa phanzi lililonse limene amatenga,sawabu imodzi imalembedwa, ndipo ulemelero umodzi umakwezedwa ndipo tchimo limodzi limachotsedwa m’buku lawo la zabwino ndi zoipa.

Mngelo amene ankayang’ana lilime lake ndi mkamwa mwake kenako anauza mngelo amene anakhala ku mapazi ake kuti, “Ndapeza lilime lake ndi pakamwa pake zili zonyowa ndi tahmiid (mawu oti Alhamdulillah), tasbiih ( Subhaanallah) ndi zikr ya Allah Talaa. Komabe, ndapeza kuti kuwerenga kwake Quraan Majiid n’kochepa.”

Mu kuyankhula kwina, mngeloyo ankatanthauza kuti ngakhale Dawuud bin Dinaar (rahimahullah) anali m’gulu la ma Muhaddithiin apamwamba wa nthawi yake, komanso anali kutumikira ma Hadith, chinthu chomwe chimasowekera m’moyo mwake chinali kuwerenga Quraan Majiid. kotero, ankadziwitsidwa za kufooka kwake kudzera mwa mngelo.

Pambuyo pake, mngelo mmodzi anauza mnzake kuti, “Nthawi yake yochoka padziko lapansi siinafike.” Atanena izi, denga la nyumba yake linatseguka ndipo angelo awiriwo anachoka, kenako denga linatsekedwanso.

Atachira, Dawuud bin Dinaar anazindikira kuti Allah adamudalitsa ndi mwayi wa moyo oti achitepo kanthu pa kufooka kwake. Motero anayamba kuwerenga Quraan Majiid kwambiri komanso kutenga nawo mbali kupeza sayansi yosiyanasiyana yokhudzana ndi Quraan Majiid.

Kuchokera pa nkhaniyi, tikumvetsa kuti Allah akafuna kudalitsa kapolo, kenako m’njira zapadera komanso zachinsinsi, Allah Talaa amamuonetsa zofooka zake ndikumupatsa tawfiiq kuti akonze moyo wake.

Kukhala ndi nthawi yozilingalira tsiku lirilonse

Tikuphunzitsidwa mu Hadith yolemekezeka kuti tikadzuka tiyenera kuwerenga dua iyi:

الْحَمْدُ لِلَّهِ الَّذِي أَحْيَانا بَعْدَ مَا أَمَاتَنَا وَإِلَيْهِ النُّشُورُ

Kuyamikidwa konse ndi kwa Allah amene watipatsa moyo pambuyo pa imfa, ndipo kwa Iye yekha ndi kumene tidzabwerere.

Mu dua imeneyi, tikukumbutsidwa kuti m’bandakucha wa tsiku lililonse latsopano, Allah Talaa amatidalitsa ndi mwayi wina wamoyo ndi mwayi okonzanso moyo wathu ndi kukonza zinthu zathu nthawi yathu isanathe.

Kotero, tsiku lililonse, munthu ayenera kufufuza moyo wake ndi kuzindikira zofooka zake. Kenako ayenera kuyesetsa kukonza moyo wake ndikukwaniritsa ufulu omwe ali nawo kwa Allah Talaa ndi chilengedwe.

Pambuyo pa swala zake zisanu za tsiku ndi tsiku, ayenera kupempha kwa Allah Talaa kuti amudalitse ndi tawfiiq kuti asunge dini m’moyo wake onse.

Mwa ma dua a masnun omwe Mtumiki (swallhu alyhi wasallam) adauphunzitsa Ummah ndi awa:

اللَّهُمَّ اجْعَلْ خَيْرَ عُمُرِي آخِرَهُ وَخَيْرَ عَمَلِي خَوَاتِيْمَهُ وَخَيْرَ أَيَّامِي يَوْمًا أَلْقَاكَ فِيْهِ

O Allah! Lichiteni gawo labwino kwambiri la moyo wanga kukhala gawo lomalizira, zochita zabwino za moyo wanga kukhala zomalizira ndisanachoke padziko lapansi, ndipo tsiku labwino kwambiri la moyo wanga tsiku limene ndidzakumane nanu.”

Tipemphe Allah Talaa atipatse tawfiiq yokonza miyoyo yathu ndi kubwera ku Sunnah ya Mtumiki (swallhu alyhi wasallam) kwathunthu ndipo Allah alipange tsiku lathu lopambanitsitsa kukhala tsiku lome tidzakumane naye.

Check Also

Munthu Olungama Kwambiri – Fudhail Bin Iyaaz Rahimahullah

Fudhail bun Iyaaz (Rahimahullah) aDali Muhaddith olemekezeka komanso oyera mtima wa m’nthawi yake. Allah Talaa …