Kuwerenga Durood Musanapange Dua

عن عبد الله بن مسعود قال إذا أراد أحدكم أن يسأل فليبدأ بالمدحة والثناء على الله بما هو أهله ثم ليصل على النبي صلى الله عليه وسلم ثم ليسأل بعد فإنه أجدر أن ينجح (المعجم الكبير للطبراني، الرقم: 8780، ورجاله رجال الصحيح إلا أن أبا عبيدة لم يسمع من أبيه كما في مجمع الزوائد، الرقم: 17255)

Hazrat Abdullah bun Mas’uud (radhwiyallahu anhu) adati: “Pamene aliyense mwa inu wafuna kupempha kwa Allah, ayambe duwa yakeyo pomutamanda ndi kulemekeza Allah ndi matamando oyenerera ukulu Wake ndi ulemerero Wake. Ndipo kenako awerenge duruud kumfunira zabwino Mtumiki (swallallahu alaih wasallam), ndipo pambuyo pake apemphe zofuna zake, popeza (kudzera mu njira iyi yochitira dua), pali kuthekera koti iye atha kupambana (mu dua yake kuyankhidwa).”

Kupanga ulendo ndicholinga chokaphunzira Hadith imodzi yokha

Sayyiduna Kathir bin Qais (rahimahullah) akulongosola kuti:

Tsiku linalake ndiri limodzi ndi Sayyiduna Abu Dardaa (Radhiyallahu anhu) munzikiti ku Damascus, padadzabwera munthu wina kwa iye nati, ‘’Eee Abu Dardaa (Radhiyallahu anhu), Ndayenda ntunda wautali kuchokera ku Madinah Tayyibah kudzafufuza Hadith imodzi kuchokera kwa inu, monga mmene ndidaphunzirira kuti inu mudamumva Mtumiki (swalallahu alyihi wasallam) mwiniwake”.

Sayyiduna Abu Dardaa Radhiyallahu anhu adamufunsa “Umagwira ntchito ku Dumascus?” Munthu uja adayankha, “Ayi (Basi Ndabwera kuchokera ku Damascus kudzaphunzira Hadith)”. Sayyiduna Abu Dardaa (radhiyallahu anhu) adamufunsa kenanso, “Ukunena zowona kuti ku Damascus ulibe ntchito yomwe umagwira?” Munthu uja adayankhanso kuti, “Ndabwera ndi mtima onse ndi cholinga chodzaphunzira Hadith imeneyi.”

Sayyiduna Abu Dardah (radhiyallahu anhu) adati: ‘’tanvetsera ndidamunva mthenga wa Allah (madalitso ndi ntendere zipite kwa iye) akunena kuti Allah amanfewetsera njira yokalowera ku jannah munthu yemwe wayenda ulendo kupita kukaphunzira maphunziro a dini, angelo amatambasura mapiko awo pansi pa mapazi ake komanso chinachirichonse chopezeka kumwamba ndi pansi (ngakhale nsomba m’madzi) zimampemphera chikhululuko kwa Allah. Kulemekezeka kwa munthu yemwe ali ndi maphunziro a Dini kuposa munthu yemwe ndiopembedza kwambiri koma alibe maphunzirowa kulingati Kusiyana kwakuwala kwa pakati pamwezi ndi nyenyezi, machehe ndi alowa mmalo a Mtumiki (madalitso ndi ntendere zipite kwa iye), aneneri sadasiye chuma komano adasiya maphunziro a dini, munthu amene waphunzira dini ndithudi ali ndi ulemerelo kuposa munthu wachuma.’’ (Sunan Abi Dawood #3641)

Check Also

Kuwerenga Durood Pamkumano

عن أنس عن النبي صلى الله عليه وسلم قال: ما من عبدين متحابين في الله …