Kuwerenga Durood musanapange Dua

عن فضالة بن عبيد قال: بينا رسول الله صلى الله عليه وسلم قاعد إذ دخل رجل فصلى فقال: اللهم اغفر لي وارحمني فقال رسول الله صلى الله عليه وسلم: عجلت أيها المصلي إذا صليت فقعدت فاحمد الله بما هو أهله وصل علي ثم ادعه قال: ثم صلى رجل آخر بعد ذلك فحمد الله وصلى على النبي صلى الله عليه وسلم فقال له النبي صلى الله عليه وسلم: أيها المصلي ادع تجب (سنن الترمذي، الرقم: 3476 وقال: هذا حديث حسن)

Hazrat Fadhaalah bun Ubaid (radhwiyallahu anhu) akufotokoza kuti nthawi ina Rasulullah atakhala pansi (mu musjid), munthu wina adalowa ndikuswali. Pambuyo poswali, munthuyo adapanga duwa nati: “E, Allah! Ndikhululukireni ndi kutsanulira chifundo chanu pa ine!” Poona momwe munthuyu adapangira duwa yake, adamuuza kuti: “Wafulumira kumphempha Allah zomwe ukufunaE, iwe musalli! Mukamaliza kuswali, mukakhala pansi kuti mupange dua, yambani ndi kumuyamika Allah monga kwayenera kutamandidwa. Kenako werenga Duroud pa ine, ndipo kenako upereke zosowa zako kwa Mulungu munthu woswali uja Atamaliza Swalah, adatamanda Mulungu adawerenga duruud (ndipo kenako adayamba kupempha zofuna zake). Atamuona munthuyu m’mene akuchitira ndikukwaniritsa miyambo yake bwino bwino) Mtumiki (swallallahu alaih wasallam) adamuuza, “Oh iwe amene ukuswali, panga duwa ndipo duwa yako ilandiridwa!”

Kulemekezedwa Ndi Allah Ta’ala Chifukwa Chochulukitsa Kuwerenga Durood

Zanenedwa zokhudza Abul Abbas, Ahmed bin Mansour (rahimahullah) kuti, atamwalira, munthu wina ochokera M’dera lotchedwa Sheeraz adamulota sheikh ameneyu, kumalotoko, Ahmed bin Mansoor adaima ku Mihraab (kuchibula) munzikiti waukulu wa M’dera limeneli la Sheeraz, adakongoletsedwa ndizovala zokongora kumutu kuli chisoti cha ufumu chomwe chidali chokongoletsedwa ndi miyala ya ntengo wapatali.

Munthu uja adamufunsa sheikh uja kuti, Allah Ta’ala wakuchengeta bwanji? Iye adayankha nati, “Allah Ta’ala wandikhululukira machimo anga, wandilemekeza, wandinveka chisoti chaulemu chaku Jannah ndipo wandidalitsanso pondiuza kuti ndikalowa ku Jannah,” munthu uja adafusanso nati, ndi ntchito iti yomwe (yomwe udachita ndikupangitsa kuti) Allah akulemekeze chonchi? Ndipo iye adayankha kuti, zonsezi ndi chifukwa chochulukitsa kuwerenga Durood. (Al-Qawlul Badee Pg.259)

Check Also

Kuwerenga Durood Pamkumano

عن أنس عن النبي صلى الله عليه وسلم قال: ما من عبدين متحابين في الله …