Zafotokozedwa kuti nthawi ina panali muazzin wina dzina lake Saalih mumzinda wa Baghdad. Ankadziwika ndi kudzipereka kwake ndipo anadalitsidwa ndi kupanga azaan kwa zaka makumi anayi (40)!
Komabe, kuyang’ana kamodzi kokha koopsa ndiko kunaononga munthuyu ndipo kunapangitsa zaka zake zonse makumi anayi zopanga azaan kukhala zopanda pake. Anagwa momvetsa chisoni ndipo umu ndi mowe zidakhalira:
Tsiku lina Swaalih ankakwera Minaarat kuti achite azaan, maso ake anayang’ana pa mwana wamkazi wa mnansi wachikhristu yemwe nyumba yake inali pafupi ndi mzikiti. Atangoyang’ana, anakopeka ndipo anam’konda.
Anafika kunyumba kwake nagogoda pakhomo. Mtsikanayo anafuwula kuchokera m’nyumbamo, “Ndani ali kumeneko?” anayankha, “Swaalih, muazzin.”
Mtsikanayo atatsegula chitseko, analowa m’nyumbamo namukumbatira. Mtsikana wachikhristu anadabwa ndipo anafuula kuti, “Anthu inu (ngati Asilamu) ndi amene anthu amawadalira, ndiye bwanji mukuchita chinyengo chonchi?”
Iye anayankha kuti, “Ndikufunadi kukhala nawe ndikukukwatira, ndipo ngati siuvomereza kukwatira nane ndikupha.”
Mtsikana uja anayankha mokwiya kuti, “Ndili okonzeka kukwatirana nawe ngati utasiya chipembedzo chako.” Nthawi yomweyo, muazzin adatuluka Chisilamu nati, “Ndikudzipatula ku Chisilamu ndi ku deen yomwe Muhammad swallallahu alaihi wasallam anabweretsa. Komabe, mtsikanayo sanakhutire ndipo anati, “Wangolankhula mawuwa kuti undithe, ukathana nane udzabwerera ku Dini yako. Kuti nditsimikizire kuti ukufunadi kukhala ndi ine, idya nkhumba.”
Mosazengereza, Swaalih anaika nkhumba mkamwa mwake ndikudya. Kenako mtsikanayo anamupempha kuti amwe vinyo, ndipo iye anatero ndi mtima onse.
Pomaliza vinyoyo anakwanirana m’maganizo mwake ndikumuledzeretsa, anayesa kumuyandikira. Komabe, iye analowa m’chipinda ndipo anatseka chitseko. Kenako anamuitana nati, “Kwera padenga la nyumba ndikudikira kuti abambo anga abwere. Akafika ndiye kuti apangitsa nikaah yathu.”
Kenako Swaalih anakwera padenga, koma chifukwa cha kuledzera, anagwa pansi ndikumwalira.
Mtsikanayo anatuluka nabisa thupi lake ndi nsalu. Pambuyo pake, abambo ake atafika ndipo iye anawauza zomwe zinamuchitikira anatenga mtembo usiku n’kuutaya mumsewu.
Pambuyo pake, anthu atamva za tsogolo la muazzin, ndi kusiya kwake Chisilamu, adataya mtembo wake pa dzala.
Kuchokera mu nkhaniyi, tikumvetsa mavuto omvetsa chisoni ndi zotsatira zomvetsa chisoni za munthu amene adaitana azaan kwa zaka makumi anayi.
Tikayang’ana nkhaniyii, tikupeza kuti kulephera kunabwera chifukwa chosateteza maso ake, ndipo mwina anali ndi chizolowezi choipa choyang’ana akazi.
Zotsatira zake ndi kuti zidamuchititsa kuti amukonde nkaziyu ndipo zidamubwerwtsera mavuto omwe tawamvawa zomwe gawo loipitsitsa kwambiri ndiko kutuluka chisilamu.
Alislaam Yeretsani mtima wanu potsatira chisilamu