Zopeka Mu Dini

Misampha iwiri ikuluikulu ya shaitaan yosocheretsera munthu ndi chuma ndi akazi. Misampha iwiriyi ndi yowononga kwambiri. Ndipo machimo ambiri omwe amachitika padziko lapansi amachokera ku misampha iwiriyi.

Rasulullah  adati “Ndithudi, dziko lapansi ndi lokoma komanso lokongola ( lokongola komanso lokopa) ndipo Allah Talaa  wakusankhani kukhala oimira padziko lapansi, kuti ayang’ane khalidwe lanu ndi machitidwe anu padziko lapansi. Kotero, samalani ndi fitnah ya dunya ( fitnah ya chuma) ndi fitnah ya akazi, popeza fitnah yoyamba ya Banu Israa’iil inali fitnah ya “akazi.”

Kupatula misampha ya chuma ndi akazi, msampha wina owopsa omwe shaitaan amagwiritsa ntchito kuwononga dini ya anthu ambiri ndi msampha wa bid’aat (machitidwe atsopano mu deen).

Check Also

Kuyamika Pa Mdalitso Okhala Ndi Moyo

Dawuud bin Dinaar anali Imaam wamkulu pankhani ya Hadith komanso mphunzitsi wa ma Muhadditheen otchuka, …