Safar (Ulendo)

Chisilamu chidapereka malamulo ndi ziletso, ma sunnah ndi aadaab (miyambo yabwino), kuti ziphunzitse munthu momwe angakhalire muzochitika ndi makhalidwe onse.

Monga momwe dini ya Chisilamu yaperekera chitsogozo kwa munthu akakhala pakhomo, yapereka chitsogozo cha momwe ayenera kuchitira akakhala pa paulendo (ulendo).

Mu kuyankhula kwina, dini ya Chisilamu ndi yatsatanetsatane, yokwanira komanso yangwiro, kotero kuti idaganizira za khalidwe la munthu nthawi zonse ndi machitidwe onse ndikumupatsa chitsogozo choyenera.

Choncho, tikupeza kuti Shariah chapereka chilolezo kwa munthu choyenda kuti aswali ma rakah awiri m’malo mwa ma rakah anayi pa swalah zomwe ziki ndi maraka anayi. Chomwechonso, Shariah chapereka chilorezo kwa munthu wapaulendo osasala kudya mu Ramadhaan, ndipo adzabweze masiku omwe sadasale Ramadhan ikadzatha.

N’zodziwika bwino kuti munthu akamayenda, nthawi zina amakakamizika kusiya tulo lake kuti afulumizitse ulendo wake ndikufika komwe akupita munthawi yake. Chimodzimodzinso nthawi zina, amakumana ndi zinthu zomwe sizikugwirizana ndi nyengo zake. Amatha kukakamizika kusiya chakudya, chakumwa ndi moyo omwe anauzolowera kwawo, kuti akwaniritse cholinga cha ulendo wake.

Choncho, Rasulullah swallallahu alaihi wasallam adatilangiza kuti munthu akakwaniritsa cholinga cha ulendo wake, ayenera kubwerera kunyumba. Rasulullah swallallahu alaihi wasallam adati,

“Kuyenda kuli ngati gawo la mavuto aku Jahannum lomwe limalepheretsa munthu kudya, kumwa ndi kugona (kuyenda kumabwera ndi zovuta, monga momwe munthu amavutikira ku Jahannum). Choncho, munthu akamaliza zolinga za ulendo wake, ayenera kubwerera ku banja lake mofulumira.”

Mwachidule, dini ya Chisilamu yapereka ma sunnats ndi ma adaab ambiri omwe munthu ayenera kuchita paulendo kuti apeze mpumulo komanso kukhala gwero la chifundo kwa ena.

Check Also

Madua Ndi Azkaar Ogonera

Dua 1 اَللّٰهُمَّ بِاسْمِكَ أَمُوْتُ وَأَحْيٰى Eh Allah! Talaa mdzina Lanu ndidzafa ndikukhala ndi moyo. …