Sunnats Ndi Aadaab Za Podzuka

1. Mukangodzuka, pukutani nkhope yanu ndi m’maso pogwiritsa ntchito manja anu onse kuti muchotse chitulotulo.

2. Mukadzuka, werengani mawu awa:

الْحَمْدُ للَّه الَّذِي أَحْيَانَا بَعْدَ مَا أَمَاتَنَا وَإِلَيْهِ النُّشُورُ

Kutamandidwa konse ndi kwa Allah yemwe watipatsa moyo pambuyo pa imfa ndipo kwa iye ndikobwelera.

3. Mukadzuka, tsukani mkamwa ndi miswaak.

Bibi Aaishah (radhiyallahu anha) akusimba kuti Nabiy (swallahu alayhi wassalam) akadzuka masana kapena usiku ankagwiritsa ntchito miswaak asanachite wudhu.

Zindikirani : Ziyenera kudziwika bwino kuti kugwiritsa ntchito miswaak ukangodzuka ndi sunnah ina komanso kugwiritsa ntchito popanga wudhu ndi sunnah inanso ngati munthu sakufuna kupanga wudhu kuti aswali atadzuka kuchokera ku tulo (kapena mkazi ali ku msambo), ndiye kuti ayenera kugwiritsa ntchito miswaak akadzuka. Komabe, ngati munthu achita wudhu nthawi yomweyo atadzuka ndikugwiritsa ntchito miswaak popanga wudhu, ndiye kuti kugwiritsa ntchito miswaak panthawi ya wudhu kudzakwanira m’malo mwa ma sunnah onse awiri.

Check Also

Sunnati Ndi Adaab 3

12. Ngati mungadzukire pakati pa usiku, werengani dua yotsatirayi ya masnun ndipo pambuyo pake mutha …