Kuikonzekera Ramadhan

21.Kudzukira kudya Dakwi kuli ndi Madalitso ochuluka (Mabaraka).kotero, kwaniritsani Sunnah ya Dakwi musanayambe kusala.

عن أبي سعيد الخدري رضي الله عنه قال قال رسول الله صلى الله عليه وسلم السحور كله بركة فلا تدعوه ولو أن يجرع أحدكم جرعة من ماء فإن الله عز وجل وملائكته يصلون على المتسحرين رواه أحمد وإسناده قوي (الترغيب والترهيب، الرقم: ١٦)

Olemekezeka Abu Saeed Khudriyy (radhiyallahu anhu) akusimba kuti, Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati: “Dakwi ili ndi madalitso ochuluka, Kotero musasiye Sunnah ya Dakwi, ngakhale wina akhoza kungomwa mkhwiko imodzi ya madzi panthawi ya Dakwi (munthu adzapanga zimenezi pongofuna kukwaniritsa Sunnah ya Dakwi komanso pofuna kupeza madalitso). Ndithudi Allah Ta’ala amapereka Chifundo chake kwa anthu onse omwe amadzukira Dakwi komanso angelo amawapemphera maduwa.”

وعن عمرو بن العاص رضي الله عنه قال قال رسول الله صلى الله عليه وسلم فصل ما بين صيامنا وصيام أهل الكتاب أكلة السحر. (صحيح مسلم، الرقم: ١٠٩٦)

Olemekezeka Amr bin Aas (radhiyallahu anhu) akusimba kuti, Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati: Kusiyana kwa swaum yathu ndi swaum ya anthu A bukhu (Ayuda ndi akhristu akale) kuli pakudya Dakwi.

22. Nthawi ya Dakwi imayambira gawo lachisanu ndi chimodzi la usiku (sixth), Komano ndi zabwino kwambiri kuchedwetsa kudya Dakwi. Komano musachedwetse mpaka kuyamba kuopera kuti mungadutsitse nthawi yake ya Dakwi.

عن أنس بن مالك رضي الله عنه أن نبي الله صلى الله عليه وسلم وزيد بن ثابت تسحرا فلما فرغا من سحورهما قام نبي الله صلى الله عليه وسلم إلى الصلاة فصلى قلنا لأنس كم كان بين فراغهما من سحورهما ودخولهما في الصلاة قال قدر ما يقرأ الرجل خمسين آية (صحيح البخاري، الرقم: ٥٧٦)

Olemekezeka Anas (radiyallah anhu) akusimba kuti, Nthawi ina Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) ndi Zaidi bin Thaabit (radhiyallahu anhu) adakhala pansi kumadya Dakwi. Koma pamene adatsiriza Dakwi, Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adaimilira kukapempheretsa Swalat ya Fajr. Anzake a Sayyiduna Anas radhwiyallahu anhu adamufunsa iye nati, Kodi pankadutsa nthawi yaitali bwanji pakati pakutsiriza Dakwi ndikuyamba kupemphera swalah ya Fajr. Sayyiduna Anas (radhwiyallahu anhu) adati, padadutsa nthawi yofanana munthu kutha kuwerenga mavesi a mu Quran okwanira makumi asanu (50).

23. Ngati wina wadzuka kuti adye dakwi akuyeneranso kupemphera swalah ya Tahajjudi.
Mwezi wa Ramadhan imam’patsanso munthu mwayi oti akhoza kupemphera swalah ya Tahajjud panthawi imene wadzuka kuti adye Dakwi.

24. Mukuyenera kumasula (kufuturu) mofulumira pamene lalowa dzuwa.

عن سهل رضي الله عنه قال: قال رسول الله صلى الله عليه وسلم: لا يزال الناس بخير ما عجلوا الفطر. قال أبو عيسى حديث سهل بن سعد حديث حسن صحيح (سنن الترمذي، الرقم: ٦٩٩)

Olemekezeka Suhail (radhiyallahu anhu) akusimba kuti, Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati ´Anthu adzapitilirabe kukhala muzabwino ngati akufulumizitsa kumasula swaum (kufuturu).

عن أبي هريرة رضي الله عنه قال : قال رسول الله صلى الله عليه وسلم قال الله تعالى أحب عبادي إلي أعجلهم فطرا. (سنن الترمذي، الرقم: ٧٠٠)

Olemekezeka Abu Hurairah (radhwiyallahu anhu) akunena kuti, Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati, Allah Ta’ala amanena kuti; Akapolo amene ali okondedwa pamanso panga ndi omwe amafulumizitsa kumasula swaum (kufuturu) nthawi yake ikakwana.

25. Ndi zabwino kwambiri kumasula swaum ndi Tende kapena madzi.

عن سلمان بن عامر قال: قال رسول الله صلى الله عليه وسلم إذا أفطر أحدكم فليفطر على تمر فإنه بركة فإن لم يجد تمرا فالماء فإنه طهور (سنن الترمذي، الرقم: ٦٥٨)

Olemekezeka Salman bin Aamr (radhiyallahu anhu) akusimba kuti, Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati “Panthawi yomasula swaum, Masulani podya Tende, chifukwa mumapeza madalitso ochuluka (mukamasula ndi tende). Koma ngati wina alibe tende akuyenera amasule pokumwa madzi chifukwa madziwo amayeretsa.

عن أنس قال : كان النبي صلى الله عليه وسلم يفطر قبل أن يصلي على رطبات فإن لم تكن فتميرات فإن لم تكن تميرات حسى حسوات من ماء (سنن الترمذي، الرقم: ٦٩٦)

Olemekezeka Anas (radhwiyallahu anhu) akusimba kuti, Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) ankamasula swaum yake ndi tende wa fureshi asadapemphere swalah ya Maghrib. Ngati Tende wafureshi palibe, Pamenepo Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) ankamasula ndi tende wouma. Ngati Tende wouma palibe Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) ankamasula swaum yake ndi mkhwiko zochepa za madzi.

26. Werengani duwa iyi panthawi yomasula (yofutulu),

اَللّهُمَّ لَكَ صُمْتُ وَعَلى رِزْقِكَ أَفْطَرْتُ فَتَقَبَّلْ مِنِّيْ إِنَّكَ أَنْتَ السَّمِيعُ العَلِيم

O Allah, Ndamanga swaum chifukwa chainu, ndipo ndi chakudya chanu ndamasula swaum yanga, Landirani swaum yangayi. Ndithudi inu ndiinu mwini kumva ndiponso ndiinu mwini kudziwa zinthu zonse.

ذَهَبَ الظَّمَأُ وَابْتَلَّتِ الْعُرُوْقُ وَثَبَتَ الْأَجْرُ إِنْ شَاءَ اللّٰهُ

Ludzu (langa) latha, ndipo misempha yanyowa, Ndipo malipiro aperekedwa (ndi Allah Taala) mukufuna kwake.

Check Also

Chikondi Cha Sayyiduna Abu Bakr (radhwiyallahu anhu) Kumukonda Nabi (sallallahu alaih wasallam)

Nabi (sallallahu alaih wasallam) adawuyamba nsamuko pamodzi ndi Abu Bakr (radhwiyallahu) anhu chakumadzulo, nkatikati mwa …