Njira Ya Sunnah Yopangira Wudhu Gawo La chisanu Nchitatu

21. Sisitani (kukhula/kutikita ndi dzanja lanu) ziwalo zanu mokwanilira pamene mukusambitsa ndicholinga choti madzi afike paliponse.

22. Ziwalo zonse ziyenera kutsukidwa china pambuyo pachinzake mosachedwetsa.

23. Pamene mukupanga wudhu musayankhule popanda chifukwa chenicheni.

24. Musaononge madzi pamene mukupanga wudhu.

عن عبد الله بن عمرو رضي الله عنهما أن رسول الله صلى الله عليه وسلم مر بسعد وهو يتوضأ فقال ما هذا السرف فقال أفي الوضوء إسراف قال نعم وإن كنت على نهر جار (سنن ابن ماجة، الرقم: ٤٢٥)

Sayyiduna Abdullah bin Amr (radhwiyallahu anhu) akunena kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adadutsa pafupi ndi Sayyiduna Sa’d (radhwiyallahu anhu) akupanga wudhu, Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) ananfunsa nati, “bwanji kuononga madzi chotere (pamene ukupanga wudhu)? iye anayankha nati, palinso kuononga madzi popanga wudhu? Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) anayankha nati “inde, ngakhale pamene ukupangira wudhu m’mbali mwamtsinje (nthawi imeneyonso ukufunika kuonetsetsa kuti siukuononga madzi).“


 

Check Also

Sunnah komanso miyambo yoyenera kutsatira usanayambe Kuwerenga Quraan Majiid 7

17. Nkosaloredwa kwa munthu yemwe ali ndi Janaabah kapena mkazi wa Haidh kuwerenga Quraan Majiid. …