Masunnah Ndi Aadaab (miyambo) Ya Pa Kusamba – Gawo 1

1. Yang’anani ku Qiblah (komwe timayang’ana tikamaswali) mukamasamba. ndibwino kuvala chovala kutchinga maliseche pamene mukusamba.[1]

2. Sambirani malo omwe wina sangakuoneni. ndibwino kusamba mutaphimba maliseche anu. komano ngati wina ali malo omwe sangaonedwe ndimunthu wina (ngati kubafa) ngati wina akusamba maliseche, ndizoloredwa.[2]

عن يعلى رضي الله عنه أن رسول الله صلى الله عليه وسلم رأى رجلا يغتسل بالبراز بلا إزار فصعد المنبر فحمد الله وأثنى عليه ثم قال صلى الله عليه وسلم إن الله عز وجل حيي ستير يحب الحياء والستر فإذا اغتسل أحدكم فليستتر (سنن أبي داود، الرقم: ٤٠١٢)[3]

Sayyiduna Ya’laa (radhiyallahu anhu) akufotokoza kuti tsiku lina, Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adamuona munthu wina akusamba pantetete kenaka Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) anakwera pa mwimbali anatamanda Allah ndikumulemekeza ,kenaka adati,’’ ndithudi Allah ndiwamanyazi(amachita ndi akapolo ake zinthu mwamanyazi kwambiri ndimwa ulemu) ndiobisika (samaoneka pamaso pa akapolo ake) amakonda (akapolo ake kuti akhale) ndimanyazi komanso kudzitchinga (pamene akudzithandiza kapena kusamba ndizina) pachifukwa ichi pamene munthu akusamba, ayenera kutchinga thupi lake.’’

3. Zingakhale bwino mutagwiritsa ntchito chidebe(chitini) posamba.[4]

4. Ngati mukusamba pa shawa, onetsetsani kuti simukuononga madzi, musadzipake sopo kapena kuchotsa tsitsi losafunikira pamene madzi ali chitsegulile, uku ndikuononga kwambiri komanso tchimo.[5]


[1] كذا يسن … الاستقبال (تحفة المحتاج 1/297)

[2] لا يجوز الغسل بحضرة الناس إلا مستور العورة فإن كان خاليا جاز الغسل مكشوف العورة والستر أفضل (المجموع شرح المهذب 2/157)

[3] سكت الحافظ عن هذا الحديث في الفصل الثاني من هداية الرواة (1/236) فالحديث حسن عنده

[4] حدثتني ميمونة قالت كنت أغتسل أنا ورسول الله صلى الله عليه وسلم من إناء واحد من الجنابة هذا حديث حسن صحيح (سنن الترمذي، الرقم: 62)

[5] اتفق أصحابنا وغيرهم على ذم الإسراف في الماء في الوضوء والغسل وقال البخاري في صحيحه كره أهل العلم الإسراف فيه والمشهور أنه مكروه كراهة تنزيه وقال البغوي والمتولي حرام (المجموع شرح المهذب 2/152)

Check Also

Ma Sunnah Komanso Miyambo Ya Dua 2

2. Popanga dua, kwezani manja anu mofanana ndi pachifuwa chanu (i.e. molingana ndi chifuwa chanu). …