Chipembedzo chachisilamu pamodzi ndi nsanamira zake chagona pa chikhulupiliro chenicheni, ngati zikhulupiliro za munthu ndizolakwika, ngakhale kuti sizingamutulutse m’chisilamu, ngakhale atachita ntchito zabwino zachisilamu, sangalandire malipiro amene Allah adalonjeza, chifukwa choti zikhulupiliro zake ndi tsinde lenileni lachisilamu ndizolakwika.
Ngati zikhulupiliro za munthu zikusemphana ndi zikhulupiliro za Dini ya chisilamu (zikhulupiliro zofunikira kwambiri zomwe zimampangitsa munthu kukhala nsilamu weniweni), ndiye kuti ngakhale atakhala ndi maonekedwe oti iyeyo ndi nsilamu ndikumatsatira zizindikiro zonse zosonyeza chisilamu pamodzi ndi asilamu enieni, chifukwa choti Sali nawo m’gulu lokhulupilira kwenikweni zachisilamu, sadzalandira sawabu (malipiro) chifukwa choti iyeyo sali nawo m’gulu la anthu okhulupilira.
Tsopano pa nkhani yokhudzana ndi munthu amene alibe chikhulupiliro, Allah Ta’ala akulongosora mu Quran yolemekezeka kuti;
مَثَلُ الَّذِينَ كَفَرُوا بِرَبِّهِمْ اَعْمَالُهُمْ كَرَمَادِ نِ اشْتَدَّتْ بِهِ الرِّيحُ فِي يَوْمٍ عَاصِفٍ ؕ لَّا يَقْدِرُوونَ مِمَّا كَسَبُوا عَلىٰ شَيْءٍ ؕ ذٰلِكَ هُوَالضَّلٰلُ الْبَعِيدُ ﴿سورة ابرٰهيم: ١٨﴾
“fanizo la amene sadakhulupilire mwa mbuye wawo (Allah) zochita zawo (zabwino zomwe sadzalipidwa nazo chabwino chilichonse chifukwa chakuti sadazichite pofuna kukondweretsa Allah) ziri ngati phulusa lomwe likuulutsidwa ndi mphepo ya nkuntho; ndipo sadzatha kupindura chirichonse pazimene adachita, uko ndikutaika konka nako kutali (ndi choonadi).
Mu ayah ina yamu Quran Allah akufotokoza:
قُلْ هَلْ نُنَبِّئُكُم بِالْاَخْسَرِينَ أَعْمَالًا ﴿١٠٣﴾ الَّذِينَ ضَلَّ سَعْيُهُمْ فِي الْحَيٰوةِ الدُّنْيَا وَهُمْ يَحْسَبُونَ اَنَّهُمْ يُحْسِنُونَ صُنْعًا ﴿١٠٤﴾ أُولٓـٰئِكَ الَّذِينَ كَفَرُوا بِاٰيٰتِ رَبِّهِمْ وَلِقَآئِهِ فَحَبِطَتْ اَعْمَالُهُمْ فَلَا نُقِيمُ لَهُمْ يَوْمَ الْقِيٰمَةِ وَززْنًا ﴿١٠٥﴾ ذٰلِكَ جَزَآؤُهُمْ جَهَنَّمُ بِمَا كَفَرُوا وَاتَّخَذُوا اٰيٰتِي وَرُسُلِي هُزُوًا ﴿سورة الكهف: ١٠٦﴾
Nena: ‘kodi tikudziwitseni za anthu oluza (olephera) pazochita zawo? Awa ndi omwe Khama lawo lataika pa umoyo wa padziko lapansi, pomwe iwowo akuganiza kuti akuchita zabwino.Iwowo ndi omwe sadakhulupilire zisonyezo zambuye wawo, ndipo (sadakhulupilire) zakukumana naye. Choncho zochita zawo zaonongeka (zapita pachabe), ndipo patsiku lachiweluzo sitidzawaikira sikelo. Zimenezo, mphoto yawo ndi Jahannam chifukwa chakusakhulupilir kwawo, ndipo aya zanga pamodzi ndi atumiki anga adachitira chipongwe.
Kuchokera m’ma Ayayh (mavesi) anenedwa pamwambawa, tikupeza kuti popanda Imaan (chikhulupiliro) siungakhale okhulupilira (nsilamu).
Zikhulupiliro Zoyenelera
Imaan kutanthauza kuti, kukhulupilira mwa mphanvu mu umodzi wa Allah Ta ‘ala komanso kukhulupilira mu mbiri zake, zakutsika kwa utumiki wa Mtumiki (Sallallahu alaih Wasallam), kukhulupilira mu utumiki wa aneneri onse alaihimu salaam, kupezeka kwa angelo, kuvumbulutsidwa kwa mabukhu onse, kukhulupilira mu Taqdeer (chikonzero), kubwera kwa tsiku la Qiyamah komanso kukhulupilira zakuukitsidwa kwa akufa, zakupezeka kwa Jannah ndi Jahannam ndizina zotero.
Ngati wina amangoswali, kupereka zakaat, kusala kudya m’mwezi wa Ramadhan, amapitanso ku Hajj ndi zina, komano samakhulupilira mu nsanamira za imaan, sadzatengedwa kuti ndi nsilamu, kotero, ndizolimbiktsidwa kwa munthu wina aliyense kuti aphunzire Dini moyenera komanso kuzindikira nthambi zofunikira za Imaan ndi cholinga choti ukhale ndi Imaan yeniyeni ndikupeza malipiro omwe adalonjezedwa Kwa ochita ntchito zabwino, ndikudziyandikitsa kwa Allah Ta ‘ala.